MAWU OYAMBA
ULIMI WA NG’OMBE ZA MKAKA
MAWU OYAMBA
Ulimi wa ng’ombe za mkaka ku Malawi kuno umapereka mkaka wochepa zomwe zimachititsanso kuti mkaka womwedwa pa munthu m’modzi aliyense uzikhala ochepa. Ndikofunika kuti tichulukitse mkaka pochulukitsa n’gombe za mkaka komanso kuthekera kwa ng’ombezi kupereka mkaka wambiri. Ku Malawi kuno ng’ombe za mkaka zochokera maiko ena zilipo ndipo zimazolowera mosavuta nyengo ya kuno. Ulimi umenewu ndi umodzi mwa ulimi omwe umathandiza kuchepetsa njala ndi kutukula miyoyo ya anthu okhala m’madera akumidzi muno m’Malawi.
Ubwino wa ulimi wa ng’ombe za mkaka
- Kupeza mkaka omwe umapereka thanzi kwa anthu
- Kupeza ndalama pogulitsa
- Kupezetsa anthu ntchito poti kuweta ng’ombe za mkaka
- Mkaka uli ndi msika osavuta
- Kupeza manyowa omwe amathandiza kuchulukitsa zokolola
- Kupeza ndiwo.
Zopinga pa ulimi wa ng’ombe za mkaka
- Kuperewera kwa chidziwitso chosamalira ana a ng’ombe kuti ng’ombe za mkaka zichulukane
- Ulimiwu umafuna kuti mlimi akhale wodziwa kayendetsedwe ka buzinesi
- Kuchepa kwa akatswiri okweretsa/kukwatitsa ng’ombe
- Kusintha kwa nyengo.