ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUCHULUKITSA/KUKWATITSA NG'OMBE ZA MKAKA

KUCHULUKITSA/KUKWATITSA NG’OMBE ZA MKAKA

Cholinga chachikulu cha ulimi wa ng’ombe za mkaka ndikupeza mkaka nthawi zonse, choncho ndikofunika kuti ng’ombe izibereka chaka ndi chaka. Msoti umatha msinkhu ukakwanitsa miyezi 7 yakubadwa. Pa nthawiyi msoti umayamba kuonetsa zizindikiro zofuna khunzi. Zizindikirozi zimaoneka masiku 21 alionse. Msoti umayenera kukweretsedwa ukakwanitsa miyezi 16 kapena pomwe wakwanitsa kulemera kwa makilogalamu 250.

Zizindikiro zofuna nkhuzi :

  • Ng’ombe sikhazikika
  • Maliseche a msoti amafufuma (kutupa), ndipo mkati mwake mumakhala monyowa komanso mofiira
  • Imaliralira komanso imakodza pafupipafupi
  • Imatuluka chikazi kumaliseche
  • Imakwera zimzake komanso imalolera kukweredwa
  • Imasala/kuchepetsa kudya kuyerekeza ndi momwe imadyera masiku onse.

Njira zokweretsera ng’ombe zamkaka

  1. Njira yachilengedwe

Iyi ndi njira yomwe nkhuzi imakwera ng’ombe ya yikazi

Ubwino wogwiritsa njira ya chilengedwe

  • Simuvutika kuyang’anira ngati ng’ombe ikufuna kukweredwa
  • Nthawi zambiri, nkhuzi siiphonya ng’ombe yayikazi yomwe ili ndi chilakolako.

Zovuta za njira ya chilengedwe

  • Ng’ombe zimakhala pa chiopsezo chachikulu chotenga matenda opatsirana pokwerana
  • Kusamala nkhuzi kumafuna ndalama zochuluka
  • Pamakhala mpata waukulu woti ng’ombe zitha kukwerana pachibale makamaka ngati simusunga ndondomeko zolondola za makweretsedwe a ng’ombe zanu.
  1. Kukweretsa ndi zida (Artificial Insemination)

Iyi ndi njira yoika umuna wang’ombe m’chiberekero cha ng’ombe yayikazi pogwiritsa ntchito zida.

Ubwino wokweretsa ndi zida

  • Mumakhala ndi ufulu osankha umuna wa nkhuzi yomwe mungayifune
  • Umuna ndi otsika mtengo kuyerekeza ndi kusunga nkhuzi
  • Njirayi imachotsa chiopsezo chopatsirana matenda pokweretsa ng’ombe
  • Ndi njira yogwiritsa ntchito mowirikiza mbewu ya nkhuzi za mphamvu
  • Mutha kugwiritsa ntchito mbewu yomwe ingapereke mwana wamkazi kapena wamwamuna.

Zovuta za njira yokweretsa ng’ombe ndi zida

  • Nchitoyi imafuna kukhala ndi upangiri woyenera
  • Imagwiritsa ntchito zida zokwera mtengo komanso zosapezeka mwachisawawa
  • Mumayenera kuti muzidziwe bwino zizindikiro za ng`ombe yomwe ikufuna nkhuzi.

Zoyenera kudziwa za kubereketsa ndi zida

  • Muyenera kuyang’anira ng’ombe modekha kawiri kapena kataku patsiku kwa mphindi makumi awiri kuti muwone ngati ikufuna kukweredwa
  • Ngati ng’ombe yayamba kuonetsa zizindikiro zofuna kukweredwa m’mawa muyikweretse madzulo atsiku lomwelo, chomwechonso ngati yayamba kuonetsa zizindikiro madzulo muikweretse m’mawa atsiku linalo
  • Ngati ndikotheka, mukhoza kukweretsa ng’ombe yanu kawiri kuti ikhale ndi mwayi wochuluka wotenga bere
  • Ngati masiku 21 adutsa mutakweretsa ng’ombe yanu ndipo zizindikiro zofuna kukweretsa sizinabwerenso, zingasonyeze kuti ng’ombeyo yatenga bere. Mungathe kutsimikiza za kutenga bere patatha miyezi itatu pogwiritsa ntchito njira yofufuzira bere
  • Nthawi zonse mulembere tsiku lomwe ng’ombe yanu ikuyenera kudzaonetsanso zizindikiro zofuna kukweredwa
  • Ng’ombe ikatenga bere imazabereka pakatha miyezi isanu ndi inayi (9)
  • Ng’ombe yanu iyenera kukweretsedwanso pakadutsa miyezi iwiri itangobereka kapena pa nthawi yomwe yaonetsa zizindikiro zofuna kukweredwa kachiwiri kuchokera pomwe yabereka.
Share this Doc