KUSAMALA THOLE KUYAMBIRA TSIKU LOBADWA MPAKA NTHAWI YOLEKANITSA NDI MAI WAKE
KUSAMALA THOLE KUYAMBIRA TSIKU LOBADWA MPAKA NTHAWI YOLEKANITSA NDI MAI WAKE
Tsiku loyamba mpaka lachinayi
- Kholo limanyambita mwana akangobadwa. Izi zimathandiza kuti mwana asabanike komaso zimathandiza kukulitsa ubale pakati pa kholo ndi mwana
- Mupake ayodini pamchombo kuti mupewe tizirombo toyambitsa matenda
- Mulore mwana (thole) kuyamwa kwathunthu mkaka woyamba (Chithuwi) masiku anayi oyambirira. Mkaka woyamba umakhala wopatsa thanzi komanso umakhala ndi asirikali oteteza thupi ku matenda. Umaperekanso michere ya protein yomwe imagaidwa mosavuta ndi kugwiritsidwa ntchito mthupi komanso umathandiza kutsegula njira yachakudya ya thole.
- Muyeze ndi kulemba kulemera kwa mwanayo.
Kulephera kuyamwa kwa thole
- Ngati thole likulephera kuyamwa bwino, mulipatse mkaka kudzera m’botolo. Mkakawu ukhale wofunda pa mulingo wa kufunda kwa thupi. Mkaka wotentha kwambiri kapena wozizira ungathe kuyambitsa matenda otsegula mmimba
- Pa nthawiyi, mkaka usakamidwe koma ngati mkaka wachuluka m’mawere, mkakawu mukhoza kukama kuti ng’ombe isavutike komanso kuti ng’ombe izathe kupereka mkaka moyenera mukuthekera kwake.
Kuleretsa mwana kwa kholo lina
- Ngati kholo lafa thole lisanalandire mkaka oyambirira, ndipo ngati pali ng’ombe ina yomwe nayonso yangobereka kumene, ndipo ikanapereka chithuwi, ipatseni mkaka umenewo
- Ngati kholo lina palibe, mupange zolowa m’malo mwa mkaka oyamba posakaniza izi:
- Dzira limodzi
- Lita imodzi yamadzi a ukhondo ndi wofunda
- Mafuta ophikira odzadza sipuni imodzi yaying’ono otchedwa cod liver
- Mafuta ansatsi odzadza masipuni atatu aang’ono.
- Izi musakanize bwino ndikumwetsa thole katatu patsiku kwa masiku anayi kenako mutha kupereka zakudya zolowa m’malo mwa mkaka.
Kuchoka pa tsiku lachinayi (4) kufika tsiku lachisanu ndi chitatu (8)
- Pakatha masiku atatu, thole litha kupatulidwa kwa kholo ndikupatsidwa mkaka tsiku lirilonse kudzera m’botolo
- Kulekanitsaku kumathandizira kuti ng’ombe ipange mkaka wina ochuluka komanso okwanira kuyamwitsa thole.
Kuchokera tsiku la nambala 8 kufika pomwe thole lidzaletsedwe kuyamwa
- Kuyambira tsiku la nambala 8 kufika mwezi umodzi wakubadwa, mwana akhoza kuyamwa kawiri pa tsiku kapena kupatsidwa mkaka okwana malita awiri m’mawa komanso masana
- Muzikama kholo kawiri patsiku ndikusiya nkhumbu imodzi kuti mwana ayamwe. Pa nthawiyi muyenera kuphunzitsa thole kudya udzu pang’onopang’ono kufikira litazolowera
- Pakutha pa masabata 12, muonetsetse kuti thole likudya udzu mokwanira ndi madeya kuti lisazavutike pa nthawi yomwe mudzaliletse kuyamwa
- Ngati thole likuoneka kuti silingalimbe palokha, muyembekezerebe kwa masiku musanaliretse kuyamwa.
Kuletsa thole kuyamwa
- Nthawi ikakwana letsani thole kuyamwa kwa mayi wake ndikuliyambitsa kudya zakudya zina osati mkaka
- Msinkhu womwe thole mukuyenera kuliletsa kuyamwa umatengera momwe mukudyetsera bwino thole lanu. Mukadyetsa bwino, thole muthanso kulirekanitsa ndi mayi wake mofulumira. Msinkhu wovomerezeka ndi miyezi itatu kapena masabata 12
- Zinthu zina zofunikira pa thole mumayenera kupanga pa nthawi imeneyi monga kuthena ndi kuchotsa nyanga
- Muyenera kuyamba kulisambitsa thole lanu ku dipi ndi kumwetsa mankhwala anyongolotsi motsatira dongosolo loyenera.