ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KULEMBERA NDI KUSUNGA ZOCHITIKA PA ULIMI WA NG'OMBE ZA MKAKA

KULEMBERA NDI KUSUNGA ZOCHITIKA PA ULIMI WA NG’OMBE ZA MKAKA 

Kuti ulimi wang’ombe za mkaka uyende bwino, pafunika kumalembera zonse zomwe zikuchitika pa ulimi wanu tsiku ndi tsiku. Zonsezi zikhale mundondomeko yomveka bwino komanso yosavuta kuitsatira. Mwazina ndondomeko zofunika kwambiri kwa mlimi wa ng’ombe za mkaka ndi monga izi:

  • Dongosolo la momwe ng’ombe zikutulutsira mkaka.
  • Dongosolo la momwe ng’ombe zazikazi zikuberekera.
  • Dongosolo la ndalama zomwe zikulowa ndi zomwe zikutuluka

Ndikofunika kwambiri kuti ng’ombe yanu iliyonse ikhale ndi chizindikiro. Izi zimathandiza kuti kalembera wanu ayende bwino.

KALEMBERA WA NG’OMBE YA MKAKA

Chizindikiro cha ng’ombe:………………………….

Tsiku lomwe yagulitsidwa/kuchotsedwa:………….

Momwe ikuonekera (Mtundu):……………

Chifukwa chake:……………………………..

Kholo lake (nkhuzi):………………………..

Mtundu wa nkhuzi:……………….

Kulemera kwa zogulitsidwa:………………………

Kholo lake (yayikazi):………………………

Mtundu wa ng’ombe yaikazi:……………….

Mtengo wa zogulitsidwa:…………………………

Tsiku lobadwa: ……………….

Kulemera kwake pa nthawi yosiyitsa kuyamwa:………..

Ndalama zonse pamodzi :…………………………

Tsiku lomwe inagulidwa:…………………

Mtengo womwe inagulidwa:…………

Kalembera wokhudza n’gombe payokhapayokha

Chaka

Zaka zake

Chizindikiro cha nkhuzi ndi mtundu wake

Chizindikiro cha thole

Tsiku lobadwa thole

Yaimuna kapena yaikazi

Kulemera kwake tsiku lobadwa

Ngati imabereka mosavuta

Kulembera kwake pa nthawi yosiyitsidwa kuyamwa

Share this Doc