ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KHOLA LA NG'OMBE ZAMKAKA

KHOLA LA NG’OMBE ZAMKAKA

Khola labwino liyenera kukwaniritsa izi;

  • Kuthandizira kugwira ziweto mukafuna kuzigwira
  • Akhale malo aukhondo ndi osavuta kusamala
  • Lipereke chitetezo ku ziweto ku mvula ndi nyengo zonse zosakhala bwino
  • Lisapereke danga kuti tizirombo toyambitsa matenda tiswane
  • Lipereke mpata woti inu eni ziweto muziyang’anire mosavuta
  • Lisapangitse kuti zakudya ziziwonongeka
  • Lipereke chitetezo ku ziweto kwa akuba ndi nyama zolusa
  • Lipereke mpata kuchotsa manyowa mosavuta.

Malo omangapo khola la ng’ombe

  • Khola likhale pamtunda wa mamita 70 ndipo lisatalikire kuposa mamita 90 kuchokera kunyumba zokhala anthu
  • Akhale malo otsetserekako kuopetsa kudikha madzi nthawi ya mvula
  • Malo ayenera kukhala kufupi ndi nyumba kuwopetsa akuba
  • Akhale malo oti ndi komwe kumapita mphepo kuchokera ku nyumba zokhala anthu kuopetsa mphepo zonukha kupita ku nyumbako
  • Mbali yotsetsereka ya khola isayang’anane komwe kukuchokera mphepo ya mkuntho
  • Pansi pa khola muyikepo simenti yolimba ndi yokhakhala
  • Alimi akulimbikitsidwa kumanga makola a n’gombe pogwiritsa ntchito zipangizo zomwe angapeze mosavuta monga mitengo. Choncho alimi akulimbikitsidwa kuchita ulimi wa mitengo kuti azipeza zipangizozi mosavuta
  • Dzenje losungamo ndowe likumbidwe pafupi ndi khola komanso lizivindikiridwa kuopetsa ntchentche ndi fungo loyipa.

Muyezo wa Khola

Khola likhale ndi malo otakasuka okwanira ng’ombe zomwe muli nazo kuti ziweto zizitha kugona kapena kudzuka komanso kutembenuka mosavuta.

  • Ng’ombe imodzi yayikulu imafuna malo okwana mamita 9.3 mbali zonse ndipo thole (mwana wa ng’ombe) limafuna malo okwana mamita 2.3 mbali zonse. Choncho ng’ombe ziwiri zazikulu zimafuna malo okwana mamita 3.7 mulifupi ndi 6.1 mulitali ndipo malowa atha kuonjezedwa pomwe nambala ya ziweto ikuonjezereka
  • Zogonera zikhale za ukhondo komanso zopereka mtidzi makamaka pamalo omwe ng’ombe zimagona kapena kupumapo
  • Denga la khola likhoza kukhala losiyanasiyana chachikulu ndichakuti ng’ombe zitetezeke kudzuwa komanso mvula
  • Zipangizo zomangira khola zikhoza kukhalanso zosiyanasiyana koma muwonetsetse kuti ziweto zikukhala mkati komanso zikutetezedwa ku zirombo zolusa.
Share this Doc