MATENDA A NKHUKU NDI ZOYENERA KUCHITA
MATENDA A NKHUKU NDI ZOYENERA KUCHITA
Chitopa
- Matenda a chitopa timayambitsa ndi tizirombo ta mtundu wa vayilasi
- Chitopa chimagwira nkhuku ya msikhu uliwonse
- Matendawa alibe makhwala ochiza
- Chofunika ndikuteteza nkhuku zisanadwale
Zizindikiro za Chitopa
- Nkhuku imatentha thupi
- Nkhuku siyimadya
- Nkhuku imapuma mobanika
- Nkhuku imapinda khosi
- Nkhuku zimachita chitosi chobiriwira
- Nkhuku imatsokomola/kukhosomola
- Nkhuku imafundira mapiko
- Nkhuku zimafa zambiri ndipo nthawi zina zimafa zonse.
Zoyenera kuchita poteteza
- Chotsani nkhuku zimene zasonyeza zizindikiro za chitopa ndi kuziyika pazokha
- Tetezani nkhuku zanu zisanadwale pozipatsa katemera
- Musalore anthu osiyanasiyana kulowa mu khola la nkhuku ndipo onetsetsani kuti olowa mkhola aponde madzi a mankhwala a mtundu wa (disinfectant) opha tizirombo
- Perekani katemera wotchedwa Lasota kapena I2 pakatha miyezi itatu kapena inayi iri yonse kuti muteteze nkhuku ku matenda a chitopa.
Gumboro
- Matenda a Gumboro timayambitsa ndi tizirombo tamtundu wa vayilasi
- Amagwira nkhuku za msinkhu woyambira tsiku limodzi mpaka masabata 8
- Matendawa amafala kudzera mu mumphweya, fumbi, zitosi, ziwiya ndi kusuntha nkhuku zodwala kapena zophedwa kuchokera malo ena kupita dela lina
- Matenda a Gumburo amatha kupha theka la khola lonse la nkhuku.
Zizindikiro za Gumboro
- Kusasangalala
- Kusadya
- Kumwa madzi ambiri mowilikiza
- Nkhuku yodwala imakhala chonyonyomala
- Nkhuku imatsegula mmimba mwa zitosi zobiriwira
- Mapiko amalendewera ndipo m’nthenga zimanyankhalala
- Nkhuku zodwala zimatha kufa masiku ochepa chidwalirireni.
Kuteteza
- Onetsetsani kuti m’khola ndi mwa ukhondo nthawi zonse
- Sesani mkhola ndi kutsukiramo makhwala opha tizirombo otchedwa formalin wa 4%
- Osalowetsanso nkhuku zina mkholamo mpaka patatha sabata imodzi
- Nkhuku zosiyana misinkhu zisawetedwe pamodzi
- Pewani kukayendera makola a anzanu
- Perekani katemera ku nkhuku zanu ndi katemera wotchedwa Bursin-2 pamene nkhuku zamaliza sabata imodzi, bwerezani pamene zamaliza sabata zitatu
- Onetsetsani kuti nkhuku zonse zodwala zachotsedwa pakati pa zina
Kamwazi wa Nkhuku
- Matendawa amagwira nkhuku zamtundu uli wonse komanso msinkhu uli onse
- Matendawa amayambitsidwa ndi tizirombo ta mtundu wa Coccidia
- Tiziromboti timagwira ndi kuswana m’matumbo a nkhuku
- Matendawa amafala kudzera muchakudya, madzi, utuchi, ziwiya, anthu kapena ziweto zina zomwe zagwedwa zitosi zokhala ndi mazira a tiziromboti.
- Tizirombo timeneti tikhoza kukhala ndi moyo mu utuchi kapena mudothi kwa chaka
Zizindikiro za Kamwazi
- Kusasangalala
- Mapiko amalendewera ndipo nthenga zimanyankhalala
- Zitosi zosakanikira ndi magazi kapena za madzimadzi
Kupewa matenda a Kamwazi
- Onetsetsani kuti mukuchita ukhondo mu khola
- M’khola mudzikhala mouma nthawi zonse
- Nkhuku zisathinane m’khola ndipo onetsetsani kuti mukusunga nkhuku zofanana misinkhu mkhola limodzi
- Perekani mankhwala otchedwa Triple Sulpher, ESB3 kapena Amprolium kwa nkhuku zimene zikusonyeza zizindikiro za matendawa
- Patulani nkhuku zodwala ndi kuzisunga pazokha.
Nthomba
- Matendawa amagwira nkhuku za msinkhu uli wonse
- Tizirombo tamtundu wa vayilasi ndito timayambitsa
- Tiziromboti timalowa mthupi la nkhuku kudzera muzironda za mkamwa, pa lipombo ndi pa gawo liri lonse la thupi
- Tiziromboti timapilira ku nyengo zouma moti titha kukhala mpaka zaka 10 munyengozi
- Matendawa amafala mwa pang’ono pang’ono ndipo atha kukhalabe mkhola mpaka miyezi itatu
Zizindikiro za Nthomba
- Amayamba ndi timatuza toyera tomwe kenako timauma nkuoneka tabulawuni pa lipombo ndi kunkhope ya nkhuku
- Pakutha pa sabata ziwiri kapena zitatu timauma
- Matendawa akakhodzokera, zizindikiro zimaoneka m’miyendo ndi mthupi lonse. Matuzawa akasupulidwa amaoneka ngati chilonda cha tsopano
- Matendawa amapha nkhuku koma osati kwambiri, komabe nkhuku zoyikira zimaikira mochepera
Kuteteza
Perekani katemera wotchedwa poxine pakati pa masabata 7 mkapa 16 akubadwa. Katemerayu amabayidwa mu phiko. Ndipo popereka katemera uzani alangizi akuthandizeni.
Chimfine
- Matendawa amayambitsidwa ndi tizirombo ta mtundu wa bakiteria
- Nthawi zambiri amatendawa amabwera mwa mphamvu kwambiri nthawi zinanso amatha kukhala nthawi yayitali m’nkhuku asanathe, koma amafala kwambiri m
- Amatupitsa gawo la kumutu ndi mphuno za nkhuku
- Tizirombo toyambitsa matendawa timalowa mthupi la nkhuku kudzera mmaso ndi mu mphuno.
- Tiziromboti timatha kukhala kunja kwa thupi la nkhuku kwa masiku awiri kapena atatu komabe sitichedwa kufa ndi kutentha.
Matendawa mungawazindikire powona izi ku nkhuku:
- Kutupa maso ndi kholingo
- kuvutika kupuma
- Kutuluka mamina onunkha
- kusiya kuikira mazira ndi
- kuyetsemula.
Choyenera kuchita tikaona chimodzi mwa zizindilirozi
- Matendawa ndi ochizika
- Kaguleni mankhwala oyenera monga Streptomycin, Dihydrostreptomycin polumikizana ndi alangizi aziweto.
Nthata za Nkhuku
Iti nditizirombo tomwe timayamwa magazi mthupi la nkhuku
Zizindikiro
- Tiziromboti timaoneka pa thupi la nkhuku
- Nkhuku zimaoneka zosowa mtendere
- Zimadzikandakanda
- Pena zimakonda kusamba mfumbi, mchenga, utuchi kapena phulusa
- Nkhuku zimaoneka zoperewera magazi mthupi ndipo lioombo limaoneka lotuwa ndi lofota
Kuteteza kwake
- Sesani mkhola tsiku ndi tsiku
- Kwa nkhuku zomwe ziri ndi nthata zithireni mankhwala otchedwa Actelic pauda ndi kuwazanso mkhola.
Njoka za m’mimba
- Nkhuku nazonso zimadwala njoka za mmimba
- Nkhuku zimagwidwa ndi njoka za m’mimba kudzera mu zakudya ndi madzi omwe agwera zitosi zokhala ndi mazira a njoka za m’mimba.
Zizindikiro za Njoka za m’mimba
- Nkhuku zimachepa magazi, zimanyentchera ndipo zimapinimbira (sizikula bwino)
- Nkhuku zoikira mazira zimasiya kuikira
- Nkhuku zimatsegula m’mimba
Zoyenera kuchita tikaona zizindikirozi
- Tizipatse mankhwala nkhuku zathu zikafika masabata 17 kenako pakapita masiku 21 kenakonso pakatha miyezi itatu iri yonse
- Kaguleni mankhwala a njoka za m’mimba kumasitolo kapena kafunseni kwa a langizi a ziweto
Kuteteza nkhuku ku Njoka za m’mimba
- Tsatirani ukhondo wa mkhola
- Perekani mankhwala opha njoka za m’mimba monga Piparazine nthawi ndi nthawi monga kumayambiliro a nyengo ya mvula ndi ku mathero a nyengo ya mvula
Tsatirani ndondomeko ya katemera kuti nkhuku zanu zitetezedwe motere:
Katemera wa nkhuku za mazira:
Katemera wa nkhuku za nyama: