ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MAKOLA A MBUZI

MAKOLA A MBUZI

Makola abwino ndi ofunikira ku chiweto china chiri chonse chifukwa:

  1. Amateteza mbuzi ku tizilombo toyambitsa matenda ndi matenda osiyanasiyana
  2. Amateteza mbuzi ku mvula, mphepo ndi dzuwa.
  3. Amatetezera mbuzi ku mbava ndi zilombo zolusa.
  4. Amathandizira kutolera ndowe zokwanira.

Zoyenera kutsatira posankha Malo omanga Khola la Mbuzi

Malo omangapo khola akhale otere:

  1. Khola limangidwe pafupi ndi nyumba zogona kuteteza mbuzi ku mbava
  2. Timange khola mbali yomwe kukupita mphepo kuti fungo kuti lisalowe m’nyumba yogona anthu.
  3. Khola likhale pa malo okwera kuti madzi adzitsetsereka.
  4. Khola likhale pa mitengo yotayana kwambiri komanso lisamangidwe pa tchire kuteteza mbuzi ku zirombo zorusa.

Chithunzi kuonetsa khola lomangidwa mbali ya kopita mphepo

Share this Doc