ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MITUNDU YA MAKOLA A MBUZI

MITUNDU YA MAKOLA A MBUZI

Pali mitundu iwiri ya makola a mbuzi;

  1. Khola la m`mwamba
  2. Khola la Njerwa kapena la Mdindo kapena Khola la pansi

Khola la m`mwamba

Khola la m`mwamba limakhala ngati momwe mukuonera chithunzi ichi:

Khola ili ndi lomwe liri lovomerezeka malingana kuti:

  1. Limateteza mbuzi ku tizirombo ndi matenda.
  2. Ndowe ndi mikodzo zimagwa pasi mosavuta.
  3. Afisi ndi zirombo zina amalephera kugwira mbuzi.
  4. Ndowe sizimavuta kuchotsa.
  5. Mkhola mumakhala mpweya wabwino chifukwa umalowa ndikutuluka mosavuta.

Mlingo wa khola la m`mwamba

  • Ngati mbuzi ziri zochepera 10, khola likhale mamita 1.8 mulifupi ndi mamita 2.8 mulitali.
  • Mbuzi zochuluka pakati pa 10 ndi 20 khola likhale mamita 2.7 mulifupi ndi mamita 3.7 mulitali
  • Kuchokera pansi kufika pa phaka kutalika ndi mita imodzi
  • Chipupa kuchokera pa phaka chikhale mamita 1.8 kulekera mamita awiri (2)
  • Mitengo yopangira phaka ikhale yowongoka bwino.
  • Mitengo ya phaka izisiyana ndi mpata wa mamirimita 20 kuti ndowe ndi mikodzo zizigwa pansi mosavuta.
  • Timange kodyeramo ku mbali ya khoma kuti udzu ndi masamba ziziyikidwa m’menemo kuopetsa kuti mikodzo ndi ndowe zisagwere ku zakudya. 

Share this Doc