KALEREDWE KA ANA A MBUZI
KALEREDWE KA ANA A MBUZI
Kuti ana a mbuzi aleredwe bwino tiyenera kutsatira izi;
- Onetsetsani kuti kamwana kayamwa mkaka oyambirira pasanathe maola 24.
- Patulani make ndi kamwana pa gulu la mbuzi kwa sabata limodzi.
- Ipatseni madzi abwino nthawi zonse.
- Ngati mukuweta mbuzi za mkaka, mupatule ka mwana kuti kaziyamwa kawiri pa tsiku
- Kapatseni kamwana ka mbuzi zakudya za udzu pakatha masiku 21.
- Thenani tiana tatimuna tonse tomwe mukuona kuti simungasunge mbewu pakatha masiku 30 (mwezi umodzi).
- Kuyambira mwezi umodzi mpaka miyezi inayi, tiana tikhoza kumakadya kutchire pamodzi ndi mbuzi zina.
- Tisamale m’khola nthawi zonse kuti tiana tisadwale.
- Tipatseni tiana mankhwala a njoka za m’mimba tikakwana miyezi iwiri komanso zina zonse mwezi umodzi mvula isanayambe, ndi mwezi umodzi mvula ikatha.
- Mbuzi zonse za bere musazipatse mankhwala a njoka za m’mimba.