ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MATENDA A MBUZI

MATENDA A MBUZI

Ngakhale mbuzi sizidwaladwala, zilinso ndi matenda ake omwe zimadwala

Kamwazi

Awa ndi matenda omwe amayamba ndi kachirombo kotchedwa Pulotozowa ndipo kamagwira matumbo

Zizindikiro zake

  1. Mbuzi siyisangalala
  2. Mbuzi siyimadya ndipo imawonda
  3. Imatsegula mmimba mwa magazi (kamwazi)

Kupewa kwake

  1. Mkhola mukhale mwa ukhondo ndi mouma nthawi zonse.
  2. Tichotse ndowe nthawi zonse ngati khola liri lapansi.

Mbuzi zodwalazo zipatsidwe mankhwala a sulfer drug.

Khunyu

Matendawa amafala kudzera ndi Nkhupakupa

Zizindikiro zake

  • Khosi la mbuzi limapindika ndikumazungulira
  • Mbuzi zimazungulira mitu
  • Mbuzi zimafa mwadzidzi
  • Mbuzi zimatsegula mmimba
  • Mbuzi zimakomoka
  • Mbuzi zimasiya kudya
  • Mbuzi zimatuluka thovu komaso malovu kukamwa

Chofunika kuchita

 Pitani kwa alangizi a ziweto kuti akuthandizeni mwa changu

Njoka za m’mimba

Zizindikiro za matendawa ndi izi:

  1. Mimba imatupa
  2. Mbuzi imatsegula m’mimba
  3. Mbuzi imatha magazi
  4. Tiana tambuzi timakhosomola or kutsokomola nthawi zina.

Kupewa kwake ndi Kuchiza:

  1. Mwetsani mbuzi makhwala a njoka za m’mimba kumayambiliro amvula ndi ku mapeto amvula.
  2. Chotsani ndowe m’nkhola la mbuzi tsiku liri lonse.
  3. Zimwetseni mbuzi mankhwala a Vabazini kapena kuzibaya Ivomeki
  4. Chitani kasinthasintha wa malo odyetsera mbuzi.

Zironda za ku Kamwa kwa mbuzi

Chomwe chimayambitsa zironda za ku kamwa :

Ka chirombo kosaoneka ndi maso ka vayilasi

Zizindikiro zake 

  • Matuza mu miromo ndi pamphuno/mfuno za mbuzi.
  • Chiweto sichidya ndipo chimawonda.
  • Matendawa amagwira mbuzi za msinkhu uliwonse

Choyenera kuchita mlimi akaona zizindikirozi: 

Matenda wa ndi ochizika. Funsani upangiri kwa alangizi a ziweto a dera lanu.

Kuola kwa Ziboda za mbuzi


Nthendayi imayamba ndi kachilombo ka Bakiteriya

Zizindikilo za matendawa ndi zironda m’ziboda komanso kutsimphina poyenda.

Kupewa kwake:

  1. M’khola mukhale mowuma nthawi zonse.
  2. Chotsani ndowe mkhola nthawi zonse.
  3. Wengani zikhadaba za Mbuzi zikakula kwambiri.

Kuchiza kwake: 

Matendawa ndi ochizika

  • Chotsani minofu yonse yoola pa chilondacho ndi kampeni
  • Thirani mankhwala ovomerezeka pa pachilonda
  • Tsukani ndikuthira mankhwala tsiku ndi tsiku mpakana chilonda chitapola.
  • Onetsetsani kuti ziweto sizikudyera ndi kukhala mmalo a matope
  • Chotsani nkhupakupa ndi minga kumapazi a mbuzi

Chibayo

Chimayamba ndi vayilasi, ndipo chimafala kudzera mmadzi, zakudya ndi zogonera za m’khola la Mbuzi. Ziweto zodwala zitha kupatsira zinzake

Zizindikiro za Chibayo cha Mbuzi: 

  1. Kutentha thupi la Mbuzi
  2. Kufowoka kwa Mbuzi
  3. Kusowa chilakolako cha chakudya
  4. Chinfine chotuluka mamina olimba ndi achikasu
  5. Manthongo mmaso a Mbuzi
  6. Mbuzi imapuma mobanika
  7. Mbuzi imatsegula mmimba
  8. Mbuzi imataya bere
  9. Mbuzi ithanso kufa pakati pa masiku 5 ndi 10.

Choyenera kuchitia mlimi akawona chimodzi mwa zizindikirozi:

  •  Funsani upangiri kwa alangizi a ziweto a dera lanu.
  • Share this Doc