MITUNDU YA NJUCHI
MITUNDU YA NJUCHI
Zunguya, mfumukazi and ogwira ntchito (source: www.pinterest.com)
Zunguya (drone)
- Iyi ndi njuchi yaimuna yomwe imagonana ndi manthu
- Thupi lake ndi lokhuthala ndi lakuda
- Ilibe mbola komanso ilibe mano
- Ili ndi maso akuluakulu
- Moyo wake imakhala masiku sikisite
- Imafa ikagonana ndi manthu kapena nthawi yanjala imantha kuphedwa ndiogwirira ntchito.
Mfumukazi / Manthu (Queen)
- Ili ndi fungo lonukhira bwino lomwe limaitana amuna.
- Mapiko ake ndioyerelako komanso atalikirako
- Khosi lake ndilokulirako ndiponso laubweya waufupi.
- Ilibe miyendo yotengela ufa.
- Imaikila mazira 2500 kapena kuposela apo pa dziku
- Moyo wake umakhala pakati pa zaka ziwiri ndi zisanu
- Mkamwa mwake mulibe mano.
- Mazira amatenga masiku atatu kuti igogomole
Ogwira ntchito (workers)
- Imaikira mazira koma sagogomola
- Ili ndi zida zonse zokwanila kugwiritsira ntchito pokatenga ufa wa mmaluwa, madzi, phula.
- Njuchi izi zimakhala ndiubweya komanso matupi ake amakha onyata
- Iyi ndiimene imagwira ntchito zones ming’oma monga; kuteteza ana anjuchi nzisa, kusamalira mabokosi momwe muli ana anjuchi, kupeza zakudya.