ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

NDONDOMEKO YOYENERA KUTSATA MUKAFIKA PA MNG'OMA PA NTHAWI YOYENDERA KAPENA KUKOLOLA

NDONDOMEKO YOYENERA KUTSATA MUKAFIKA PA MNG’OMA PA NTHAWI YOYENDERA KAPENA KUKOLOLA

Musanafike Pa Mng’oma

  • Muyime kaye patali ndi kuvala zovala zoyenera (bee suit)
  • Muwonetsetse kuti chofukizira utsi chikuyaka bwino ndipo kuti muli ndi zoyatsira zokwanira. Kawirikawiri zoyatsira zabwino ndi ndowe zang’ombe kapena zitsononkho ndipo onetsetsani kuti zikhale zouma
  • Fikani pa mng’oma kudzera kumbuyo osati kutsogolo kumene kuli khomo.

Pa Mng’oma

  • Munthu amene ali ndi chofukizira utsi ndi amene apite kutsogolo kwa mng’oma
  • Poperani utsi mu mng’oma
  • Atagwira ntchito yopopera utsi mu mng’oma, munthuyo achoke ndikupita kumbuyo kumene kuli anzake kuti nawo apeze mpata ogwira ntchito.

Zosayenera Kuchita Mukafika Pa Mng’oma

  • Osatsekula mng’oma popanda chifukwa koamnso osasiya mng’oma wotseguka nthawi yayitali
  • Osafika pa mng’oma ndi chofukizira utsi chimene sichikuyaka bwino
  • Osagwiritsa ntchito moto oyaka kuopa kuotcha njuchi
  • Osafika pafupi ndi mng’oma musanavale -zovala zozitetezera
  • Osayima kutsogolo kwa mng’oma
  • Osapanga phokoso pamene mukugwira ntchito pa mng’oma
  • Osapita kumene kuli ming’oma ya njuchi mutadzola kapena kunyamula mafuta wonunkhira (perfurme)
  • Osatsegula ming’oma nthawi ya usiku
  • Osavala zovala za ubweya komanso zokhwepa pa mng’oma
  •  Osagwiritsa ntchito matayala, machubu, makatoni amene adatengeramo zinthu za poizoni
Share this Doc