KUKOLOLA NDI KUKONZA MASAMBA A CHAM'MWAMBA
KUKOLOLA NDI KUKONZA MASAMBA A CHAM’MWAMBA
Kukolola Masamba
- Pakatha miyezi pakati pa 6 ndi 12, mitengo imakhala ndi masamba amene angathe kukololedwa
- Sambani m’manja ndi sopo polimbikitsa ukhondo
- Kololani masamba a cham’mwamba dzuwa lisanakwere, monga m’mamawa kapena madzulo
- Pamene tikukolola tiwonetsetse kuti m’masamba mulibe mame ngakhalenso madontho a madzi; chifukwa masamba a mame amakawola tikakasunga kapena ponyamula zokolola
- Pokolola masamba, dulani tinthambi ting’onoting’ono mosaononga mitengo
- Pokolola masamba kuchokera pa mitengo imene ikadali yaying’ono, monga ya miyezi isanu ndi umodzi kapena kukolola pa nthambi zimene zaphukira pa chitsa cha mitengo ya cham’mwamba, ndi kofunika kukolola pogwiritsa ntchito mpeni wokuthwa kapena chisikiro. Dulani pa mulingo woyenerera, monga kusiya masentimita 30 kuchoka pansi; kapenanso kusiya mita imodzi pansi ndi kuchotsa nthambi
- Nyengo yabwino kukolola cham’mwamba ndi miyezi ya Epulo kapena pamene mvula yangotha kumene.
Kukolola masamba a cham’mwamba
Kuyanika Masamba Amene Akololedwa
Tisayanike masamba padzuwa. Kuyanika pa dzuwa kumachotsa michere yofunikira ku thanzi komanso pochiza matenda. Choncho, tisanakolole, tikuyenera kumanga choyanikira choyendera mphamvu ya dzuwa. Timange choyanikira kufupi ndi kumene kuli munda wa mitengo ya cham’mwamba kupewa kuwononga masamba ndi zinthu zina zosowa ukhondo. Pogwiritsa ntchito choyanikirachi timateteza masamba ku fumbi ndi zinthu zina zimene zingawononge masamba athu kuti asinthe maonekedwe/ kolite. Choyanikira choyendera mphamvu ya dzuwa chimatenga maola ochulukirapo powumitsa masamba, kusiyana ndi kuyanika pa dzuwa, kumene kumatenga maola ochepa koma mowononga . Alimi akulimbikitsidwa kuyanika masamba a cham’mwamba ndi choyanikira choyendera mphamvu ya dzuwa kuti akhale ndi maonekedwe abwino / kolite ya pamwamba.
Kumanga choyanikira choyendera mphamvu ya dzuwa
Ngati palibe choyanikira choyendera mphamvu ya dzuwa, mlimi amange mathandala okhala ndi denga. Ngati denga liri la udzu, ayike pepala la pulasitiki mkati mwake kupewa udzu kugwera mu masamba a cham’mwamba. Tiwonetsetse kuti pepala la pulasitiki lakwanira mkati mwa denga monse. Dziwani kuti kuyanika kumeneku kumatenga masiku ochulukirapo chifukwa kumadalira mpweya kuti uzungulire mkatimo nkuwumitsa masamba. Koma masamba ake amakhala a maonekedwe abwino.
Kusankha ndi Kusunga Masamba Owuma
Pamene masamba a cham’mwamba awuma, sankhani pochotsa masamba amene asali a mtundu woyenera monga udzu, tinthambi ta mtengo ndi zinthu zina zimene zingaononge maonekedwe/ kolite ya masamba a cham’mwamba. Masamba onse akhale obiriwira. Onetsetsani kuti ukhondo ukutsatidwa posankha masamba monga; malo akhale osesa bwino, opanda fumbi, pasakhale ziweto zirizonse, kusamba m’manja ndi sopo tisanayambe komanso tikamaliza kusankha, kugwiritsa ntchito zipangizo za ukhondo ndi zina.
Sungani masamba a cham’mwamba osankhidwa bwino m’masaka opita mphepo. Sungani pa malo owuma, pa mthunzi komanso popanda chinyontho ndi mpweya onyowa. Ikani masaka pamwamba pa mitengo yosanjidwa bwino kapena ma paleti.
Kusankha masamba owuma a cham’mwamba
Kugaya ndi Kusunga Masamba a Cham’mwamba
Tingathe kugaya masamba a cham’mwamba pogwiritsa ntchito ka chigayo kakang’ono ngakhalenso pogwiritsa ntchito mtondo ndi musi. Onetsetsani kuti pa malo amene mukugayira masamba a cham’mwamba ndi pa ukhondo, zipangizo zonse zikhalenso za ukhondo komanso ife ngati ogaya tikhalenso a ukhondo. Sungani masamba ogaya (ufa wa masamba a cham’mwamba) aja m’mabotolo, m’masacheti kapena m’matumba m’mene simulowa mpweya kapena mphepo.
Kugaya masamba a cham’mwamba Masamba a
cham’mwamba ogaya (ufa wa masamba)
Sungani ufa wa masamba a cham’mwamba m’mabotolo a pulasitiki, masacheti, mapepala a pulasitiki ngakhalenso mabotolo a galasi.
Alimi akulimbikitsidwa kudya cham’mwamba kuti akhale athanzi komanso agulitse wina kuti apeze ndalama. Ana, makamaka ochepera zaka zisanu, apatsidwe phala lothira cham’mwamba kuti akule ndi thanzi loyenerera; popezamo michere yoteteza ku matenda, yowonjezera chitetezo m’thupi, yowonjezera magazi komanso yolimbitsa mafupa.