ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MISIKA

MISIKA

Katundu opangidwa kuchokera ku cham’mwamba, makamaka ufa wa masamba, umagulitsidwa m’dziko lino m’masitolo ogulitsa mankhwala, zipatala za mankhwala a zitsamba (herbal clinics), malo okwelera ma basi komanso malo othira mafuta a galimoto. Ufa wa masambawu umagulitsidwa m’mabotolo kapena m’masacheti a 250 g komanso 500g.

Pakadali pano mafuta a cham’mwamba sagulitsidwa wamba m’dziko lino. Palinso mwayi ogulitsa katundu wochokera ku cham’mwamba ku mayiko akunja. Katundu wopita ku mayiko akunja akuyenera kuyikidwa m’matumba olemera makilogalamu 10, 25 kapenanso 50. Ndikofunikanso kulumikizana ndi ogula kuti alongosole m’mene mungalongedzere katundu, malinga ndi kukonda kwawo. Ndondomeko ina ya m’mene tingagulitsire katundu wochokera ku mitengo ya cham’mwamba tingayipeze ku Unduna wa za Malonda.

Tiwonetsetse kuti talemba bwinobwino komanso moyenerera pa mabotolo, masacheti ngakhalenso matumba a ufa wa masamba, njere, mafuta ndi katundu wina. Pamene tikulemba, tilembepo izi: dzina la katundu, kulemera kwake kwa katundu, zimene ziri mkati mwa botolo, sacheti ngakhalenso thumba, dzina la opanga ndi nthawi imene katundu wathu angathe kugwiritsidwa ntchito. Choncho, ndikofunikanso kufunsa ogula ngati pali zinthu zina zimene angafune kuti ziwonjezeredwe polemba pa mabotolo, masacheti komanso matumba. 

Share this Doc