UBWINO
UBWINO
A. Pa Zachuma
Zinthu zopangidwa kuchokera ku malambe monga; ufa wamalambe, mafuta, masamba, luzi la mkati mwa chigoba, nkhuni kuchokera ku chigoba ndi luzi lochokera ku khungwa lake zili ndikuthekera kowonjezera chuma kwa alimi. Izi zitha kuthandiza kuchepetsa alimi kudalira ku ulimi wamvula.
Ufa Wa Malambe
Mafuta a Malambe
Masamba a Malambe
Nkhuni zopangidwa kuchokera ku chigoba
B. Ku chilengedwe
- Mitengo yake imapereka mnthuzi kunthaka
- Kugwa ndikuola kwamasamba kumapereka manyowa komaso kukonza nthaka
- Imathandiza kayendedwe ndikasungidwe kamadzi munthaka
- Mabowo opezeka munthambi zake amakhala zisa zambalame komanso njuchi
C. Ku Zaumoyo ndi thanzi
Malambe ali ndiubwino osiyanasiyana kuthupi lamunthu
i. Masamba owuma
- Amathandiza ku matenda osiyanasiyana
- Masambawa amaperekanso michere ina yofunikanso mthupi la munthu
ii. Masamba a nthete
- Gwero lopezekeratu la vitamin A ndi C. Amadyedwa ngati ndiwo za masamba komanso popanga msuzi
iii. Ufa
- Muli vitamini C komanso michere ina yofunika mthupi ngati ayironi, kasiyamu, potaziyamu, komanso zothandiza kugaya chakudya mthupi.
Ufa wa malambe