KASAMALIDWE KA ZOKOLORA
KASAMALIDWE KA ZOKOLORA
- Kololani malambe atawuma bwino ndi kuyika mu nkhokwe
- Mangani nkhokwe yotalika masentimita 50 kuchoka pansi ndipo mangilani mpanda otalika osachepera mita imodzi (masentimita 100)
- Khoma likhale ndi mipata kuti mphepo izilowa mosavuta kupewa chuku
- Ikhale yaikulu bwino kuti mulu wa malambe usamatalike kopsyola 60 cm kuchoka pa phaka
- Isayandikane ndi chimbudzi, bafa, makola aziweto ndi khitchini
- Ikhale kochokera mphepo osati kopita mphepo
- Imangidwe molimba kuti igwire ntchito zaka zambiri pa malo osadikha madzi
- Ikhale ndi denga losathonya kuti chuku chisayambike chifukwa cha mvula
- Ikhale ndi chitseko kuteteza ku ziweto monga nkhuku ndi mbuzi
- Isapoperedwe ziphe (mankhwala ophera tizilombo) mwanjira iriyonse
- Onetsetsani kuti mpanda/khoma likhale ndi mipata kuti dzuwa komanso mphepo izifika pa zipatso kupewa chuku
Nkhokwe
Kuphwanya Malambe
- Onetsetsani kuti nyumba imene mukusweramo malambe ikhale yosapoperedwapo makhwala. Fufuzani mbiri ya m`mene mankhwala agwiritsidwira ntchito pa nyumbayo
- Panyumba pakhale posamalidwa bwino, pasakhale zinyalala
- Panyumba pakhale mpanda kuteteza ku ziweto
- Mazenela ayenera kutsekedwa ndima ukonde.
Musanaphwanye chipatso chamalambe onetsetsani kuti muli ndi zinthu izi:
- Chikwanje
- Mphasa yaukhondo kapena yatsopano
- Matumba oyikamo, aukhondo kapena atsopano
- Ndowa yamadzi
- Thandala loyikapo zipatso musanaziphwanye
- Zovala zodzitetezera kuphatikizapo chophimba pakamwa ndi mphuno.
- Pepala la pulasitiki yotalika mita imodzi kuti iziyikidwa kumiyendo kwanu pophwanya malambe.