ULIMI WA MPUNGA
ULIMI WA MPUNGA
MAU OYAMBA
Mpunga ndi mbewu yomwe isali ya mguru lanyemba komano yofunikira kwambiri m’Malawi muno. Mpunga ndi chakudya chimene anthu a m’madera amene umalimidwa komanso m’matawuni amadalira. Mpunga umabweretsa ndalama pa khomo la mlimi komanso kwa anthu a bizinesi ambiri. Mpunga umagulitsidwanso maiko akunja ndi anthu ochita malonda ndi kupindula.
Malimidwe a Mpunga
- Mpunga umalimidwa munyengo ya mvula komanso ya dzuwa munjira yothirira, umalimidwa malo otsika komanso okwera nthawi ya mvula komanso malo otsika nthawi ya chilimwe mumasikimu anthirira chifukwa mpunga umafuna madzi ochuluka
- Zitsanzo za masikimu amene mpunga umalimidwa kwambiri ndi monga Ku Hara, Bua, Lifuwu, Wovwe, Likangala, Domasi, Nkhate ndi ena ambiri.
- Zitsanzo za madera a Kumtunda ndi monga ku Mchinji, Mzimba (Mbawa) ndi Chitipa (Kameme).
- Dothi la makande kapena la dongo ndi limene mpunga umachita bwino chifukwa limasunga madzi kwa nthawi yotalikirapo mvula ikagwa.
- Njira zosiyanasiya zosamaririra nthaka, ziweto, zakhalango komanso zam’madzi pofuna kuthana ndi vuto lakusowa kwa zakudya komanso kusintha kwa nyengo (CSA) kuthaso kupangitsa mbewuyi kuchita bwino kwa nthawi yaitali.