ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KASAMALIDWE KA ZOKOLORA

KASAMALIDWE KA ZOKOLORA

  • Kololani malambe atawuma bwino ndi kuyika mu nkhokwe
  • Mangani nkhokwe yotalika masentimita 50 kuchoka pansi ndipo mangilani mpanda otalika osachepera mita imodzi (masentimita 100)
  • Khoma likhale ndi mipata kuti mphepo izilowa mosavuta kupewa chuku
  • Ikhale yaikulu bwino kuti mulu wa malambe usamatalike kopsyola 60 cm kuchoka pa phaka
  • Isayandikane ndi chimbudzi, bafa, makola aziweto ndi khitchini
  • Ikhale kochokera mphepo osati kopita mphepo
  • Imangidwe molimba kuti igwire ntchito zaka zambiri pa malo osadikha madzi
  • Ikhale ndi denga losathonya kuti chuku chisayambike chifukwa cha mvula
  • Ikhale ndi chitseko kuteteza ku ziweto monga nkhuku ndi mbuzi
  • Isapoperedwe ziphe (mankhwala ophera tizilombo) mwanjira iriyonse
  • Onetsetsani kuti mpanda/khoma likhale ndi mipata kuti dzuwa komanso mphepo izifika pa zipatso kupewa chuku

Nkhokwe

Kuphwanya Malambe

  • Onetsetsani kuti nyumba imene mukusweramo malambe ikhale yosapoperedwapo makhwala. Fufuzani mbiri ya m`mene mankhwala agwiritsidwira ntchito pa nyumbayo
  • Panyumba pakhale posamalidwa bwino, pasakhale zinyalala
  • Panyumba pakhale mpanda kuteteza ku ziweto
  • Mazenela ayenera kutsekedwa ndima ukonde.

Musanaphwanye chipatso chamalambe onetsetsani kuti muli ndi zinthu izi:

  1. Chikwanje
  2. Mphasa yaukhondo kapena yatsopano
  3. Matumba oyikamo, aukhondo kapena atsopano
  4. Ndowa yamadzi
  5. Thandala loyikapo zipatso musanaziphwanye
  6. Zovala zodzitetezera kuphatikizapo chophimba pakamwa ndi mphuno.
  7. Pepala la pulasitiki yotalika mita imodzi kuti iziyikidwa kumiyendo kwanu pophwanya malambe.

Share this Doc