KUDZALA MALAMBE
KUDZALA MALAMBE
Pali njira ziwiri zodzalira malambe monga kugwiritsa ntchito mapando ndi nazale.
Kusamalira Kwa Nazale
Zoyenera kutsata posankha malo ofesa mitengo (Nazale):
- Malo akhale athyathyathya osadikha madzi, ngati palibe malo a choncho konzani kuti akhale a athyathyathya
- Malo apafupi ndimadzi
- Malo otetezeka kupewa mphepo yambiri
- Malo omwe sangakokoloke
- Malo omwe sanagwidwepo ndi tidzilombo towononga mbewu
- Otetezedwa kudziweto
Nazale ya malambe
Kufesa mbewu ku nazale
- Wiritsani madzi, phulani ndikunyika njere zanu kwa mphindi 30
- Khadabulani pang`ono njere ndi chowengera zala , mpeni kapena poyikhulitsa pa mwala
- Dzalani mbewu imodzi kapena ziwiri mumachubu mumaenje olowa sentimita imodzi kapena masentimita awiri
- Thirirani kamodzi madzulo mpaka zitamera
- Mbeu zikatuluka pakapita masabata awiri, pamafunika kuthirira m`mawa ndi madzulo koma ngati kunja kukutentha kwambiri mukuyenera kuthirira madzulo okha
- Thirirani mpaka miyezi itatu kenako mutha kukadzala ku nkhalango.
Nthangala za malambe