MALAMBE
MALAMBE
Malambe ndi mtengo wachilengedwe wokhala ndi chithunthu
chachikulu,chimene chimakhala ndi nthambi zing’onozing’ono zobala zipatso zokhala
mzikamba. Kutalika kwake amatha kufika mamita 25 komanso kunenepa kwake pakati pa mamita 6 ndi
10. Masamba
ake amakhala olezekalezeka pasanu ndiofanana ngati zala za mchikhatho.
Mlambe umamera bwino kumalo kwa nyengo yotentha. Ku Malawi kuno malambe amapezeka maboma monga awa: Mangochi, Machinga, Salima, Nsanje, Karonga, Rumphi, Chikwawa, Balaka, Dedza, Ntcheu ndi Neno.