MISIKA
MISIKA
a) Misika ya komkuno
Misika yomwe imagula zochokera ku malambe opanda kuzisintha kapena kuonjezera maonekedwe aliwonse. Misika yambiri m`Malawi muno ndiyotero. Anthu ambiri amagwiritsa ntchito malambe popanga zakumwa (filizesi ndi juwisi) kapena masuwiti.
Juwisi wa malambe
b) Misika ya malambe ya kunja
Misika ya kunja makamaka amafuna ufa kapena mafuta a malambe a oganiki (organic).
Malambe a oganiki ndi chiyani? Malambe a oganiki ndi amene amatoledwa ku nkhalango kumene kulibe minda yothiridwa fetereza kapena mankhwala ophera tizirombo mu mbeu ndipo pamafunika maphunziro apadera kuti mupeze chiphaso chovomerezeka pa msika wa oganiki.