NDONDOMEKO ZOTSATILA POTETEZA MALONDA
NDONDOMEKO ZOTSATILA POTETEZA MALONDA
Vulani nsapato pophwanya malambe
Onetsetsani kuti simukudwala amodzi mwamatenda awa:
- Chimfine
- Kutsegula mmimba
- Kusamza
- Matenda apakhungu monga mphere
- Matenda amaso
- Matenda amakutu
- Chizungulire
- Kukhosomola kulikonse
- Matenda a chiwindi
- Matenda ena alionse opatsilana
Ndondomeko Zina Zofuna Kutsatira
- Musadzole zonunkhilitsa thupi kapena mafuta onunkhila kwambiri
- Musagwilitse ntchito sopo onunkhila kwambiri
- Musavale ma wotchi, mphete kapena ndolo
- Valani zovala zopanda mabatani monga ma tisheti kapena Malaya opanda ma batani
- Ma foni a mmanja atalikile malo ogwilira ntchito
- Musavale zovala mnkhosi kapena zibangili ndizina zotero
Mosungira Malambe Ophwanya
- Mukaphwanya malambe onetsetsani kuti mwasunga matumba anu pa malo osanja bwino kutetezera ku chinyontho ndi chiswe.
- Matumba asagunde khoma pakhale mpata wa masentimita 50 ndipo pansi pakhale mpata wa masentimita 30.
- Nyumba ikhale ndi zitseko zokhoma kutetezera ziweto ndi akuba.