KALIMIDWE KA MTENGO WA CHAM'MWAMBA
KALIMIDWE KA MTENGO WA CHAM’MWAMBA
MAWU OYAMBA
Cham’mwamba amapezeka kwambiri m’madera a m’mphepete mwa njanya ya Malawi komanso ku chigwa cha mtsinje wa Shire. Mitengo ya cham’mwamba imakula mwachangu kwambiri, ndi yopilira ku chilala komanso imakula bwino m’madera osowa madzi. Komabe, mtengo umenewu umakula m’madera onse, kungoti umakula bwino kwambiri m’madera otsika kuyerekeza ndi m’madera okwera.
Mtengo wonse wa cham’mwamba uli ndi ntchito yake; chimene chili chinthu chabwino kwambiri, makamaka m’madera amene anthu amadalira mitengoyi pa umoyo wawo.
Cham’mwamba uli ndi mayina ambiri potengera ziyankhulo zosiyanasiyana, monga:
Chichewa: Cham’mwamba, Kangaluni
Yao: Kalokola
English: Moringa, Horseradish Tree, Drumstick Tree, Ben oil Tree
Sena: Nsangoa
Kafukufuku wambiri wakhala akupangidwa pa mtengo wa cham’mwamba, makamaka pa masamba, zitheba komanso mafuta. Kafukufuku yense akusonyeza kuti masamba a cham’mwamba ali ndi michere yochuluka zedi yotetezera komanso kulimbana ndi matenda m’matupi athu. Masambawa alinso ndi michere yokulitsa yochuluka (amino acids), chimene chili chinthu chosowa makamaka ku masamba ndi zomera zina.
Masamba awisi a cham’mwamba ali ndi michere yochepa kuyerekeza ndi masamba owuma chifukwa pogaya masamba owuma pamakhala masamba ochuluka amene amayikidwa pamodzi. Koma masamba owuma samakhala ndi mchere wochuluka wa Vitamin C. Cham’mwamba ali ndi michere monga yoteteza ku matenda, yolimbitsa mafupa, yowonjezera magazi, yolimbana ndi matenda ena ogwira ziwalo za mkati, wokulitsa, kutsuka mthupi ndi matenda ena ambiri. Cham’mwamba ndi mtengo othandiza kwambiri popereka thanzi loyenerera kwa amayi oyembekezera komanso amayi oyamwitsa, ndipo mwana wobadwayo amalandira nawo thanziro asanabadwe komanso pamene akuyamwa. Ana onyentchera apatsidwe phala lotendera ndi ufa wa masamba a cham’mwamba ndipo thanzi lawo limabwerera. Thirani masipuni ang`ono awiri kapena atatu a ufa wa cham’mwamba mu phala la ufa, phala la mpunga ngakhalenso mu tea.
Masamba awisi a Moringa
Zitheba zaziwisi za Moringa