KUDULIRA MITENGO YA CHAM'MWAMBA
KUDULIRA MITENGO YA CHAM’MWAMBA
- Mitengo ikakula kufika pa mita imodzi, dulani masentimita khumi (10cm) ku nsonga ya nthambi pogwiritsa ntchito zida zokuthwa bwino
- Duliraninso pamene nthambiyi yakula kufika mamita 1.5 komanso mamita 2 ndi mamita 2.5. Kudulira kumeneku kumathandiza kuti mitengo ipange nthambi zochuluka, choncho masamba ndi zitheba nazo zimachuluka. Mitengo imakhala yayifupi choncho pokolola sipamakhala vuto la kutalika kwa mitengo ndipo nthawi yomweyo masamba amakhala akukololedwa
- Ngati nthambi sizikuduliridwa, mitengo imatalika kwambiri koma ili ndi nthambi zochepa; choncho timakolola masamba ndi njere zochepa.
Mitengo ya cham’mwamba yodulira nthambi