KUDZALA
KUDZALA
Kubzala Mitengo ya Cham’mwamba Kuchoka ku Njere
Njere za cham’mwamba zimamera bwino kwambiri. Tingathe kupeza njerezi potolera m’madera amene muli mitengo yake, kapena kugula ku Land Resource Centre, Forestry Research Institute of Malawi, FRIM, kapena m’malo ena ovomerezedwa ndi boma. Ngati tikutolera njere pazokha, tisankhe zitheba zimene zakula bwino komanso kuchoka m’mitengo imene yabereka bwino. Njere yabwino ndi imene yakhwima komanso kuwuma ikadali pa mtengo. Njere zikhale zofanana m’mawonekedwe ake, kulemera kwake komanso mtundu wake. Mbewu isakhalenso ndi zinyalala monga miyala, tinthambi ta mitengo, nthenga, masamba, njere zowonongeka ndi zina.
Nazale ya mitengo ya cham’mwamba ikhazikitsidwe m’miyezi ya Sepitembala mpakana Okutobala, motere:
- Sakanizani dothi la kuda kapena limene si la makande ndi manyowa komanso mchenga. Thirani dothi limeneli m’machubu ndikuthira madzi. Ngati dothi laphwera m’machubumo, onjezerani dothi linathirani, m’machubu onse
- Fesani njere imodzi kapena ziwiri mu chubu. Dzenje lofeserapo lisapitilire 2cm kuzama kwake. Kwirirani ndi dothi
- Thirirani machubu onse mukamaliza kufesa njere
- Dulirani mizu mbande zikafika masabata atatu. Dulirani mizu ponyamula machubu kawiri pa sabata mpaka patatsala masiku awiri kuti mukawokere mbandezo
- Thirirani machubu kawiri pa tsiku, m’mawa ndi madzulo kwa masabata anayi oyambilira, kenako thirirani kamodzi pa tsiku
- Khwimitsani mbande pakatsala masabata atatu mpakana anayi kuti mbande ziokeredwe. Khwimitsani mbande poyamba kuthirira ngati kuli kofuna kutero.
Dothi la m’machubu likhale ndi chinyezi koma lisakhale lonyowa. Njere zimamera pasanathe masabata awiri. Mbande zikatha sabata imodzi, patulirani kuti mu chubu chirichonse mutsale mbande imodzi. Okerani pamene mbande zafika masentimita 60 mpakana 90 komanso ziri ndi mtengo wokhwima.
Njira ina ndiyobzala njere kumunda posayika pa nazale. Njere zobzala m’munda osayika pa nazale zimakula mwachangu; koma ngati tikubzala m’munda, tibzale pamene mvula ikupita ku mapeto.
Njere zabwino
Njere zoyipa
Kubzala Kuchokera ku Nthambi
Mitengo imakula mwachangu kwambiri ngati tabzala kuchokera ku nthambi. Ndikofunika kubzala nthambi m’munda osayika pa nazale. Gwiritsani ntchito nthambi zokhwima bwino. Podula nthambi, onetsetsani kuti khungwa lake silikusupulidwa ponyamula kapena kusunga. Tikadula nthambi zoti tikabzale, tizisiye kaye pa mthunzi powuma bwino kwa masiku atatu, kenako tikabzale.
Bzalani m’maenje amene dothi lake lasakanizidwa ndi manyowa.
Nthambi zobzala zikhale zotalika masentimita 45 mpakana 150 ndipo ndi mphipi masentimita 10 mpakana 15. Maenje obzalamo nthambi akhale ozama pafupifupi theka la theka (1/3 ) m’mene nthambi yatalikira ndipo bzalani nthambyo. Pothirira, onetsetsani kuti madzi sakuchuluka kwambiri.
Kuthirira
Mitengo ya cham’mwamba siifuna madzi ochuluka. Choncho thirirani moyenerera m’miyezi iwiri yoyamba kenako thirirani pokhapokha ngati mitengo ikufunika madzi.