ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUKOLOLA NDI KUKONZA NJERE ZA CHAM'MWAMBA

KUKOLOLA NDI KUKONZA NJERE ZA CHAM’MWAMBA

  • Kololani zitheba zikawuma. Tisachedwe kukolola chifukwa zimasweka ndipo njere zimagwera pansi
  • Tikakolola tiyanikenso padzuwa kwa masiku awiri. Titsegule zitheba zowumazo nkuchotsamo njere ndi manja
  • Sungani njerezo m’masaka pa malo popita mphepo, popanda chinyezi komanso pa mthunzi. Njerezi zingathe kusungika kwa zaka ziwiri popanda vuto lirilonse, ndipo zikadzalidwa, zimamera.

Kukonza Njere za Cham’mwamba

Njere za cham’mwamba zimagwiritsidwa ntchito popangira mafuta. Mafuta a cham’mwamba asungidwe mosapitirira miyezi isanu ndi umodzi (miyezi 6) chifukwa amawonongeka mwachangu. Choncho, alimi akulimbikitsidwa kupanga mafuta okhawo amene angagwiritsidwe ntchito kapena kugulitsa popanda otsala.

Tingathe kupanga mafuta a cham’mwamba pogwiritsa ntchito makina oyendera magetsi kapenanso osayendera magetsi. Akatswiri amene amakonza makina osiyanasiyana angathenso kupanga makina owengera mafuta kuchokera ku njere za cham’mwamba. Sungani mafuta amene mwawenga m’mabotolo kapena ndowa zosamala bwino komanso malo owuma bwino. 

Share this Doc