KUSANKHA MALO OBZALAPO MITENGO YA MORINGA
KUSANKHA MALO OBZALAPO MITENGO YA MORINGA
- Akhale malo a dothi lopanda makande komanso lopanda mchenga wochuluka.
- Mvula ikhale yochuluka pa mulingo wa pakati pa mamilimita 900 mpaka 1300 pa chaka.
- Pewani kubzala pa malo pamene chiswe chimavuta.
KUKONZA MALO OBZALAPO CHAM’MWAMBA
- Sosani pa malo/munda
- Limani potipula kuti nthaka ifewe
- Mapando atalikirane motere:
- Ngati tidzakolole njere, mapando atalikirane mamita awiri mulitali komanso mulifupi
- Ngati tidzakolole masamba, mapando atalikirane mamita awiri mulitali ndipo mita imodzi mulifupi
- Kumbani maenje ozama masentimitala 30 kapena lula m’modzi. Ngati tibzalenso mbewu zina pakati pa mapando a cham’mwamba, mapando a cham’mwamba atalikirane mamita anayi (4m) potengera mtundu wa mbewu umene tizabzale
- Sakanizani dothi limene mwakumba ndi manyowa; kenako libwenzeretseni mu dzenje.