KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
Tizilombo timene timagwira cham’mwamba ndi monga; akangaude, chiswe ndi ziwala. Tetezani mitengo ya cham’mwamba popanga izi:
- Nyikani masamba a nimu kapena wombwe m’madzi kwa tsiku limodzi; ndipo poperani madziwo mu dothi lozungulira mitengo.
- Wazani phulusa kuzungulira pansi pa mitengo.
- Malo onse ozungulira komanso pakati pa mitengo ya cham’mwamba akhale opanda udzu .
- Ukhondo wa m’munda ndi ofunikira kwambiri. Udzu, tinthambi towuma komanso zonse zowuma zichotsedwe mozungulira mitengo yathu.
Dziwani izi: Kupopera mankhwala si kololedwa pa ulimi wa mitengo ya cham’mwamba pokhapokha ngati tizilombo tachuluka kwambiri. Ngati tizilombo tachuluka kwambiri, gwiritsani ntchito mankhwala amene amapha tizilombo pompopompo; akhale mankhwala amene samalowa mkati mwa zigawo za mtengo kuti kaonekedwe/ kolite ya cham’mwamba isasinthe.