UBWINO WA MTENGO WA CHAM'MWAMBA/MORINGA
UBWINO WA MTENGO WA CHAM’MWAMBA/MORINGA
- Mitengo ya Cham’mwamba ili ndi michere yochuluka yofunikira mthupi, kwa ana ochepera zaka zisanu, ana amene akukula, amayi oyembekezera ngakhalenso kwa anthu amene amagwira ntchito zolemetsa
- Cham’mwamba ali ndi michere imene imathandiza kupewa komanso kuchiza matenda ena
- Cham’mwambaamapezetsa ndalama
- Mtengo wa Cham’mwamba umathandiza kusefa mpweya
- Komanso amathandiza kupha tizirombo toyambitsa matenda m’madzi akumwa. (Njere zophwanya za moringa zimakhala ndi mphamvu yomata ku tizirombo mwa chilengedwe. Zikamata ku tizirombo zimapita pansi choncho madzi amakhala abwino kumwa)
- Amathandiza kuteteza nthaka
- Ndi chipangizo popangara sopo
- Njere za moringa zimagwiritsidwa ntchito popanga mafuta. (Mafuta amenewa amagwiritsidwa ntchito ku mafakitale opanga zakudya, mankhwala komanso mafuta okongoletsa tsitsi ndi khungu, ndi zina).
- Masamba ake amagwiritsidwa ntchito ngati tiyi wa mankhwala
- Mitengo ya Cham’mwamba imathandiza kutchinga mphepo, kupewa kukokoloka kwa nthaka.,
- Mtengo wa Cham’mwambaumatha kubzalidwa ngati maluwa
- Tingathe kubzala mtengo wa Cham’mwambandi mbewu zina kuti uthandize kupereka mthunzi wochepa ku mbewu, makamaka zimene sizifuna mthunzi wochuluka.