KUBEREKETSA/KUCHULUKITSA
KUBEREKETSA/KUCHULUKITSA
Kusankha Mbewu (Mbuzi Zoyenera Kuweta)
Mfundo izi ndi zomwe mlimi ayenera kutsatira kuti akhale ndi mbewu yabwino yoti ikhoza kumupindulira nsanga:
- Asankhe mbuzi yapanda chirema ngakhale iri yokula msinkhu.
- Asankhe mbuzi za zikuluzikulu.
- Asankhe atonde amiyendo yamphamvu komanso yolimba.
- Asankhe mtundu umene umabereka mapasa kuti zichuluke msanga.
- Athene atonde ena onse otsala kapena kuwagulitsa
- Tonde osankhidwayo akhale oberekedwa kwina osati m’kola lomwero.
- Atonde akhoza kusinthidwa pakatha chaka chimodzi, ziwiri kapena zitatu.
- Tonde mmodzi wang`ono amafunikira mbuzi 30 zazikazi pamene wamkulu amafunika mbuzi 60 zazikazi.
- Mbuzi yayimuna imayamba kubereketsa ikakwana miyezi 5-6, pamene yayikazi miyezi 10-12.
- Tonde akakwana miyezi 8-9 ndiye kuti wakhwima bwino.
- Bere la mbuzi yayikazi limatenga masiku 144-152 (5 months).
Zizindikiro zoti mbuzi yayikazi ikufuna tonde
- Mbuzi yayikazi imaliralira
- Mbuzi yayikazi imakwera zinzake ndipo imalora kukweredwa ndi zinzake.
- Imatulukanso chikazi
- Imakodza pafupipafupi
- Siyikhala ndi chilakolako cha chakudya
- Imagwedezagwedeza mchira
- Maliseche amawoneka ngati atupa komanso amaoneka ofiwira.
Pamene mbuzi yatulutsa chikazi cha magazi ndiye kuti nthawi yoti nkukweredwa ndi tonde yadutsa
Mbuzi yayikazi yomwe iri m’nyengo yofuna tonde ikukweredwa