KUSUNGA KAUNDULA WA MBUZI
KUSUNGA KAUNDULA WA MBUZI
Mlimi wa dongosolo amayenera kusunga kaundula (ma rekodi) a ulimi wake. Izi zimathandiza kuti:
- Mlimi adziwe nsinkhu wa mbuzi zake (Zaka).
- Mlimi adziwe kuchuluka kwa chakudya choti asunge kapena kufutsa malingana ndikuchuluka kwa mbuzi zake.
- Mlimi amadziwanso kuti ndi mbuzi ziti zomwe zaswa/ zabereka ana.
- Amadziwaso kuti ndi mbuzi iti imene imapereka mkaka kwambiri
- Mlimi amadziwa nthawi yomwe mbuzi yake yakweredwa ndi nthawi yoti idzabereke
- Nthawi yopereka mankhwala ku mbuzi zake
- Amadziwaso matenda omwe amavuta mderalo.