MATENDA A MBUZI
MATENDA A MBUZI
Ngakhale mbuzi sizidwaladwala, zilinso ndi matenda ake omwe zimadwala
Kamwazi
Awa ndi matenda omwe amayamba ndi kachirombo kotchedwa Pulotozowa ndipo kamagwira matumbo
Zizindikiro zake
- Mbuzi siyisangalala
- Mbuzi siyimadya ndipo imawonda
- Imatsegula mmimba mwa magazi (kamwazi)
Kupewa kwake
- Mkhola mukhale mwa ukhondo ndi mouma nthawi zonse.
- Tichotse ndowe nthawi zonse ngati khola liri lapansi.
Mbuzi zodwalazo zipatsidwe mankhwala a sulfer drug.
Khunyu
Matendawa amafala kudzera ndi Nkhupakupa
Zizindikiro zake
- Khosi la mbuzi limapindika ndikumazungulira
- Mbuzi zimazungulira mitu
- Mbuzi zimafa mwadzidzi
- Mbuzi zimatsegula mmimba
- Mbuzi zimakomoka
- Mbuzi zimasiya kudya
- Mbuzi zimatuluka thovu komaso malovu kukamwa
Chofunika kuchita
Pitani kwa alangizi a ziweto kuti akuthandizeni mwa changu
Njoka za m’mimba
Zizindikiro za matendawa ndi izi:
- Mimba imatupa
- Mbuzi imatsegula m’mimba
- Mbuzi imatha magazi
- Tiana tambuzi timakhosomola or kutsokomola nthawi zina.
Kupewa kwake ndi Kuchiza:
- Mwetsani mbuzi makhwala a njoka za m’mimba kumayambiliro amvula ndi ku mapeto amvula.
- Chotsani ndowe m’nkhola la mbuzi tsiku liri lonse.
- Zimwetseni mbuzi mankhwala a Vabazini kapena kuzibaya Ivomeki
- Chitani kasinthasintha wa malo odyetsera mbuzi.
Zironda za ku Kamwa kwa mbuzi
Chomwe chimayambitsa zironda za ku kamwa :
Ka chirombo kosaoneka ndi maso ka vayilasi
Zizindikiro zake
- Matuza mu miromo ndi pamphuno/mfuno za mbuzi.
- Chiweto sichidya ndipo chimawonda.
- Matendawa amagwira mbuzi za msinkhu uliwonse
Choyenera kuchita mlimi akaona zizindikirozi:
Matenda wa ndi ochizika. Funsani upangiri kwa alangizi a ziweto a dera lanu.
Kuola kwa Ziboda za mbuzi
Nthendayi imayamba ndi kachilombo ka Bakiteriya
Zizindikilo za matendawa ndi zironda m’ziboda komanso kutsimphina poyenda.
Kupewa kwake:
- M’khola mukhale mowuma nthawi zonse.
- Chotsani ndowe mkhola nthawi zonse.
- Wengani zikhadaba za Mbuzi zikakula kwambiri.
Kuchiza kwake:
Matendawa ndi ochizika
- Chotsani minofu yonse yoola pa chilondacho ndi kampeni
- Thirani mankhwala ovomerezeka pa pachilonda
- Tsukani ndikuthira mankhwala tsiku ndi tsiku mpakana chilonda chitapola.
- Onetsetsani kuti ziweto sizikudyera ndi kukhala mmalo a matope
- Chotsani nkhupakupa ndi minga kumapazi a mbuzi
Chibayo
Chimayamba ndi vayilasi, ndipo chimafala kudzera mmadzi, zakudya ndi zogonera za m’khola la Mbuzi. Ziweto zodwala zitha kupatsira zinzake
Zizindikiro za Chibayo cha Mbuzi:
- Kutentha thupi la Mbuzi
- Kufowoka kwa Mbuzi
- Kusowa chilakolako cha chakudya
- Chinfine chotuluka mamina olimba ndi achikasu
- Manthongo mmaso a Mbuzi
- Mbuzi imapuma mobanika
- Mbuzi imatsegula mmimba
- Mbuzi imataya bere
- Mbuzi ithanso kufa pakati pa masiku 5 ndi 10.
Choyenera kuchitia mlimi akawona chimodzi mwa zizindikirozi: