MITUNDU YA MAKOLA A MBUZI
MITUNDU YA MAKOLA A MBUZI
Pali mitundu iwiri ya makola a mbuzi;
- Khola la m`mwamba
- Khola la Njerwa kapena la Mdindo kapena Khola la pansi
Khola la m`mwamba
Khola la m`mwamba limakhala ngati momwe mukuonera chithunzi ichi:
Khola ili ndi lomwe liri lovomerezeka malingana kuti:
- Limateteza mbuzi ku tizirombo ndi matenda.
- Ndowe ndi mikodzo zimagwa pasi mosavuta.
- Afisi ndi zirombo zina amalephera kugwira mbuzi.
- Ndowe sizimavuta kuchotsa.
- Mkhola mumakhala mpweya wabwino chifukwa umalowa ndikutuluka mosavuta.
Mlingo wa khola la m`mwamba
- Ngati mbuzi ziri zochepera 10, khola likhale mamita 1.8 mulifupi ndi mamita 2.8 mulitali.
- Mbuzi zochuluka pakati pa 10 ndi 20 khola likhale mamita 2.7 mulifupi ndi mamita 3.7 mulitali
- Kuchokera pansi kufika pa phaka kutalika ndi mita imodzi
- Chipupa kuchokera pa phaka chikhale mamita 1.8 kulekera mamita awiri (2)
- Mitengo yopangira phaka ikhale yowongoka bwino.
- Mitengo ya phaka izisiyana ndi mpata wa mamirimita 20 kuti ndowe ndi mikodzo zizigwa pansi mosavuta.
- Timange kodyeramo ku mbali ya khoma kuti udzu ndi masamba ziziyikidwa m’menemo kuopetsa kuti mikodzo ndi ndowe zisagwere ku zakudya.