ULIMI WA MBUZI
ULIMI WA MBUZI
Mbuzi zimawetedwa ndicholinga chopeza nyama, mkaka ndi ndalama.
Ubwino wa ulimi wa mbuzi
- Sizidwaladwala
- Zimachita bwino ngakhale mvula igwe yochepa popeza zimadya masamba osati udzu
- Sizivuta kudyetsa ndipo mbuzi zisanu ndi imodzi zimadya malo amene ngombe imodzi imadya ndi kukhuta
- Ulimi wambuzi sufuna ndalama zambiri poyerekeza ndi ng’ombe
- Zimaberekana ndikuchulukana msanga
- Umalowetsa zochepa pa ulimiwu
- Nyama yambuzi imadyedwa ndi anthu ambiri ndipo palibe miyambo kapena chipembedzo chimene chimaletsa kudya kapena kuweta mbuzi
- Mbuzi sivuta malonda kuyerekeza ndi ziweto zina
- Ulimi wa mbuzi umabweretsa ndalama ukagulitsa
- Umapezetsa manyowa mosavuta zikasungidwa bwino mkhola
- Mbuzi zimaphedwa pa maukwati, maliro mosavuta ndiponso kulipira mirandu.
Ziwopsyezo pa ulimi wa mbuzi
- Alimi amalandira uphungu wochepa pa mbuzi zomwe zimachepetsa phindu pa ulimiwu
- Alimi akasowa ndalama amapha ndi kugulitsa mbuzi zikuluzikulu zoyenera kuweta kusiya zokwinimbira chifukwa chopelewera uphungu wa kawetedwe ka mbuzi.
- Alimi amaluza tiana tambiri tambuzi chifukwa chosadziwa kaleredwe kake.
- Alimi amaweta mbuzi opanda cholinga chenicheni chifukwa chosaphunzitsidwa bwino phindu la ulimi wa mbuzi.
- Alimi sadziwa matenda a mbuzi kotero amalephera kuziteteza zikadwala.