ZAKUDYA NDI KADYETSEDWE
ZAKUDYA NDI KADYETSEDWE
Chakudya chenicheni cha mbuzi ndi masamba komanso udzu. Ina mwa mitengo yomwe masamba ake ndi chakudya chambuzi ndi iyi:
- Nsangu
- Mpalankhanga
- Mango
- Malayina
- Nimu
- Lukina
- Gilisidiya
- Udzu wa nsenjere
- Lodzi
- Buricheria
Tisunge mfutso ngati chakudya choonjezera monga madeya ndi masangwe a mtedza.
Kufunika Kwa Zakudya zowonjezera
- Zimathandiza kuti mbuzi zipange mkaka komanso nyama wambiri.
- Zimathandizanso kuti mbuzi ziberekane kwambiri.
Nthawi yopanga zakudya zowonjezera
Mukangokolora ngati mukugwiritsa ntchito zotsala za kumunda.
Ngati mukugwiritsa ntchito udzu, pangani pamene wayamba kupanga maluwa.
Mungapange bwanji chakudya chowonjezera
- Ngati ali mapesi kapena masangwe awumitseni kaye.
- Zikauma, sungani mu mitolo (mabelo) pa mthunzi.
- Ngati ali madeya (gaga), umitsani ndikusunga m’matumba.
- Pangani chakudya china chowonjezera, posakaniza madeya (gaga) 6.9kg, lukina (tifotetse kaye) 3.0 kg, mchere 0.1kg.
Chakudya chimenechi, tipereke patsiku motere: