CHAKUDYA CHA NG'OMBE ZA MKAKA NDI KADYETSEDWE
CHAKUDYA CHA NG’OMBE ZA MKAKA NDI KADYETSEDWE
Ng’ombe za mkaka ndizofunikira chakudya chabwino kuti zikhale ndi moyo wabwino, zikule, zipereke mkaka komaso kuti ziberekane. Chakudya cha ng’ombe cha tsiku ndi tsiku chiyenere kukhala ndi zinthu izi :
- Chakudya chopatsa mphamvu (Carbohydrates)
- Chakudya chokulitsa / chomanga thupi (Proteins)
- Michere (Minerals): Iyi ndi michere yomwe yikuyenera kukhala mu gawo la chakudya cha ng’ombe za mkaka nthawi zonse. Ng’ombe zomwe mumazipatsa zakudya zoti muli michereyi zimapereka mkaka wochuluka.
- Madzi: Madzi ndi gawo lofunika kwambiri ku moyo wa ng’ombe za mkaka kuti zikupatseni mkaka ochuluka. Kuchuluka kwa madzi kutengera msikhu wang’ombe yanu ndi m’mene kunja kuliri. Ng’ombe imodzi imamwa madzi a mlingo okwana pakati pa malita 80 mpaka 100 patsiku. Ng’ombe yomwe ikupereka mkaka, lamulo ndi lakuti pa lita imodzi iliyonse yamkaka, ng’ombe yanu muyipatse madzi osachepera malita 5. Mwachitsanzo, ng’ombe yokuti ikupereka mkaka okwana malita 20 muyenera kuipatsa madzi okwana malita 100 patsiku.
Pali magulu awiri a zakudya za ng’ombe za mkaka omwe ndi udzu ndi chakudya chosakaniza (chogaya).
-
Udzu
- Ichi ndi chakudya chomwe muonetsetse kuti chikhale chochuluka poti ndichotsika mtengo komanso chopezeka mosavuta kuchokera ku mapesi, udzu komanso masangwe a mtedza ndi soya. Chakudyachi chimapezeka chobiriwira komanso chouma.
- Alimi akulimbikitsidwa kubzala udzu ndi zomera zina zokhala ndi michere yopatsa thanzi monga nsenjere ndi lukina.
- Alimi akulimbikitsidwa kusunga chakudya cha n’gombe munyengo ya dzinja pamene chimakhala chochuluka kuti adzagwiritse ntchito munyengo ya chirimwe pomwe chimasowa.
- Alimi akulimbikitsidwanso kukolola madzi a mvula m’makomo mwawo.
- Pofuna kulola kuti udzu odyetsa ng’ombe uzikula bwino, alimi akulimbikitsidwa kumasinthasintha dambo lodyetsera ng’ombezo.
-
Chakudya Chosakaniza (Chogaya)
- Ichi ndi chakudya chomwe chimakhala ndi zopatsa mphamvu ndi kukulitsa. Zitsanzo za chakudyachi ndi monga; madeya a chimanga, ufa wa chimanga, madeya a tirigu, ufa wa mapira, masese, madeya a mpunga komanso ufa wa soya
- Mungatheso kugula zakudyazi ku malo omwe amapanga ndi kugulitsa zakudya monga dairy mash ndi calf mash.