KUCHULUKITSA/KUKWATITSA NG'OMBE ZA MKAKA
KUCHULUKITSA/KUKWATITSA NG’OMBE ZA MKAKA
Cholinga chachikulu cha ulimi wa ng’ombe za mkaka ndikupeza mkaka nthawi zonse, choncho ndikofunika kuti ng’ombe izibereka chaka ndi chaka. Msoti umatha msinkhu ukakwanitsa miyezi 7 yakubadwa. Pa nthawiyi msoti umayamba kuonetsa zizindikiro zofuna khunzi. Zizindikirozi zimaoneka masiku 21 alionse. Msoti umayenera kukweretsedwa ukakwanitsa miyezi 16 kapena pomwe wakwanitsa kulemera kwa makilogalamu 250.
Zizindikiro zofuna nkhuzi :
- Ng’ombe sikhazikika
- Maliseche a msoti amafufuma (kutupa), ndipo mkati mwake mumakhala monyowa komanso mofiira
- Imaliralira komanso imakodza pafupipafupi
- Imatuluka chikazi kumaliseche
- Imakwera zimzake komanso imalolera kukweredwa
- Imasala/kuchepetsa kudya kuyerekeza ndi momwe imadyera masiku onse.
Njira zokweretsera ng’ombe zamkaka
- Njira yachilengedwe
Iyi ndi njira yomwe nkhuzi imakwera ng’ombe ya yikazi
Ubwino wogwiritsa njira ya chilengedwe
- Simuvutika kuyang’anira ngati ng’ombe ikufuna kukweredwa
- Nthawi zambiri, nkhuzi siiphonya ng’ombe yayikazi yomwe ili ndi chilakolako.
Zovuta za njira ya chilengedwe
- Ng’ombe zimakhala pa chiopsezo chachikulu chotenga matenda opatsirana pokwerana
- Kusamala nkhuzi kumafuna ndalama zochuluka
- Pamakhala mpata waukulu woti ng’ombe zitha kukwerana pachibale makamaka ngati simusunga ndondomeko zolondola za makweretsedwe a ng’ombe zanu.
- Kukweretsa ndi zida (Artificial Insemination)
Iyi ndi njira yoika umuna wang’ombe m’chiberekero cha ng’ombe yayikazi pogwiritsa ntchito zida.
Ubwino wokweretsa ndi zida
- Mumakhala ndi ufulu osankha umuna wa nkhuzi yomwe mungayifune
- Umuna ndi otsika mtengo kuyerekeza ndi kusunga nkhuzi
- Njirayi imachotsa chiopsezo chopatsirana matenda pokweretsa ng’ombe
- Ndi njira yogwiritsa ntchito mowirikiza mbewu ya nkhuzi za mphamvu
- Mutha kugwiritsa ntchito mbewu yomwe ingapereke mwana wamkazi kapena wamwamuna.
Zovuta za njira yokweretsa ng’ombe ndi zida
- Nchitoyi imafuna kukhala ndi upangiri woyenera
- Imagwiritsa ntchito zida zokwera mtengo komanso zosapezeka mwachisawawa
- Mumayenera kuti muzidziwe bwino zizindikiro za ng`ombe yomwe ikufuna nkhuzi.
Zoyenera kudziwa za kubereketsa ndi zida
- Muyenera kuyang’anira ng’ombe modekha kawiri kapena kataku patsiku kwa mphindi makumi awiri kuti muwone ngati ikufuna kukweredwa
- Ngati ng’ombe yayamba kuonetsa zizindikiro zofuna kukweredwa m’mawa muyikweretse madzulo atsiku lomwelo, chomwechonso ngati yayamba kuonetsa zizindikiro madzulo muikweretse m’mawa atsiku linalo
- Ngati ndikotheka, mukhoza kukweretsa ng’ombe yanu kawiri kuti ikhale ndi mwayi wochuluka wotenga bere
- Ngati masiku 21 adutsa mutakweretsa ng’ombe yanu ndipo zizindikiro zofuna kukweretsa sizinabwerenso, zingasonyeze kuti ng’ombeyo yatenga bere. Mungathe kutsimikiza za kutenga bere patatha miyezi itatu pogwiritsa ntchito njira yofufuzira bere
- Nthawi zonse mulembere tsiku lomwe ng’ombe yanu ikuyenera kudzaonetsanso zizindikiro zofuna kukweredwa
- Ng’ombe ikatenga bere imazabereka pakatha miyezi isanu ndi inayi (9)
- Ng’ombe yanu iyenera kukweretsedwanso pakadutsa miyezi iwiri itangobereka kapena pa nthawi yomwe yaonetsa zizindikiro zofuna kukweredwa kachiwiri kuchokera pomwe yabereka.