KUSAMALA NG'OMBE ZA MKAKA
KUSAMALA NG’OMBE ZA MKAKA
- Kudyetsera mwapadera ng’ombe ya bere
Iyi ndi ndondomeko yopereka chakudya chapadera monga chosakaniza kwa ng’ombe ya bere yomwe yatsala ndi miyezi iwiri kuti ibereke. Izi ndizofunika chifukwa zimathandiza kuti:
- Mwana akule mofulumira komanso akhale wathanzi
- Mkaka uzakhale ochuluka panthawi yomwe mwana akubadwa
- Kholo likhale lathanzi.
- Zizindikiro zoyandikira kubereka
- Ng’ombe siikhazikika
- Maliseche ake amafufuma ndipo imayamba kutulutsa chikazi
- M’mbali momerera mchira mumakhwefuka
- Pomwe kwatsala masiku awiri kuti mwana abadwe, bere limafufuma ndipo mkaka umatuluka mukakama nkhumbu.
- Kukonzekera ng’ombe kubereka
- Muonetsetse kuti ng’ombe iberekere pa malo ouma ndi osamalidwa bwino, otetezedwa ku mphepo yoomba, dzuwa, mvula komanso zirombo zolusa
- Muonetsetse kuti mwaika zogonera zokwanira bwino kuti mwana abadwire pa malo a mtidzi
- Muonerere ndi chidwi komanso mutakhala kufupi ndi ng’ombeyi kuti muthe kuthandizira pomwe ng’ombeyi ikulephera kubereka. Mwachitsanzo, Kubereka movutika pa zifukwa zina (Dystocia)
- Muonetsetse ngati kholo likulephera kunyambita mwana, muyenera kuthandizira kuchotsa zokuta mwana ku mphuno kwake
- Mwana obadwayo atetezedwe ku zirombo zolusa
- Musaisokoneze ng’ombeyi ikamabereka
- Muitane alangizi a ziweto akudera lanu ngati padutsa ola limodzi mwana asanabadwe kuchokera pomwe ng’ombeyi yayamba kubereka.