ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MALONDA A MKAKA

MALONDA A MKAKA

  • Ku Malawi kuno mkaka umagulitsidwa m’masitolo akuluakulu ngakhalenso m’misika ina yovomerezeka.
  • Alimi a ng’ombe za mkaka akulimbikitsidwa kukhala m’magulu omwe ali ndi zipangizo zosungira mkaka. Mkaka ukafika pa malowa umayezedwa ngati uli wosaonjezera zinthu zina ngati madzi, ufa komanso ngati sunaonongeke. Ngati sunapezeke ndi zifukwa umayikidwa m’malo osungira mkaka kuti uzizira. Mkakawu umagulitsidwa kwa makampani ogula mkaka omwe amalipira ma guluwa mwezi ndi mwezi kulingana ndi mkaka umene wagudwa mwezi umenewo. Mamembala a gulu losonkhelana mkaka amayenera kukhala ochokera pa mtunda osadutsa 8Km kuti mkaka uzikafika msanga usanaonongeke. Ubwino osonkhelana mkaka ndiwakuti alimi amakhala ndi kuthekera kogulitsa mkaka wawo ku ma kampani, amathanso kukhazikitsa mitengo mogwirizana pa gulu, ndiponso amatha kugula zipangizo za ulimi wa ng’ombe za mkaka pa mtengo otsika.
Share this Doc