MATENDA NDI TIZIROMBO TA NG'OMBE ZA MKAKA
MATENDA NDI TIZIROMBO TA NG’OMBE ZA MKAKA
MATENDA
ZIZINDIKIRO
KUPEWA NDI KUTETEZA
Kutupa kwa Mawere Kowonekeratu
(Clinical Mastitis)
- Tizidutswa ta magazi owundana mu mkaka ochokera ku ng’ombeyo
- Bere limatentha ndipo limatupa
- Imatentha thupi
- Imathamanga magazi
- Chilakolako cha chakudya chimachepa
- Madzi a m’thupi amachepa
- Ng’ombe imaoneka yosachangamuka
- Imatha kufa kumene.
- Perekani mankhwala ku ng’ombe nthawi yoti sizikupereka mkaka komanso ku ng’ombe za matenda a mgonamgona a kutupa kwa bere
- Tsatirani njira zaukhondo zokamira mkaka ndi ukhondo wa pamalo omwe ng’ombe zimakhala makamaka kumapeto a nyengo yomwe ng’ombe sizikupereka mkaka.
Kutupa kwa Mawere Kosaonekeratu
(Subclinical Mastitis)
- Apa kusinthika kwa bere ndi mkaka sikumawonekeratu.
- Ng’ombe imatulutsa mkaka wochepa
- Mu bere mumapezeka tizirombo totchedwa bacteria ndipo asilikali a m’thupi amawonjezereka m’magazi.
- Perekani mankhwala ku ng’ombe nthawi yoti sizikupereka mkaka komanso ku ng’ombe za matenda a mgonamgona a kutupa kwa bere
- Tsatirani njira zaukhondo zokamira mkaka ndi ukhondo wa pamalo omwe ng’ombe zimakhala makamaka kumapeto a nyengo yomwe ng’ombe sizikupereka mkaka.
Matenda a kugwa a Ng’ombe za Mkaka
(Milk Fever)
- Kutsalira kwa matumbo ovindikira mwana wang’ombe pobadwa.
- Kuchepa kwa chilakolako cha chakudya
- Ng’ombe imakhala chigonere
- Kupinda khosi ndikuyang’ana kumbuyo
- Ng’ombe imapanga chimbudzi cha ndowe zowuma
- Thupi lake limazizira
- Ng’ombe imasiya kubzukula
- Imatha kufa ngati siyinathandizidwe mwamsanga.
- Chepetsani mlingo wa mchere wa calcium mu zakudya kufika magalamu osaposera 100 pa n’gombe iliyonse patsiku makamaka kumapeto a nyengo yomwe ng’ombe sizikupereka mkaka.
- Perekani chakudya chokhala ndi mchere wa magnesium kuti mlingo wa mchere wa calcium wa m’magazi ukhale oyenera.
Matenda a Kutentha Kwathupi a Gombe Laku Mmawa
(East Coast Fever)
- Kuchepa kwa chilakolako cha chakudya
- Imaoneka yosachangamuka ndi yodwalika
- Kutentha kwa thupi mpaka 42oC
- Imapuma mwa befu
- Imatsekula m’mimba
- Kutupa kwa anabere a m’makutu, a mkhwapa ndi mphechepeche
- Imadwala kwa sabata imodzi ndipo imafa koma nthawi zina imachira pang’onopang’ono.
- Ngombe zomwe ndi za chi Malawi zisambitsidwe dipi kawiri pa mwezi makamaka nyengo ya dzinja pamene kumakhala nthata zambiri. Ngati zili zachizungu zipititsidwe ku dipi sabata iliyonse
- Ngati mlimi angakwanitse, zipatsidwe katemera wa matendawa yemwe mungampeze ku vetenale ku Lilongwe. Msinkhu wabwino kuzipatsa katemerayu ndi pomwe zinakali matole.
Matenda Odzadzitsa Madzi M’thumba la Mtima (Heartwater)
- Chiweto chimangopezeka chitafa
- Ziweto zotsalazo zimasiya kudya, zimatentha thupi ndiponso zimatsekula m’mimba
- Ziweto zimawonetsa zizindikiro zokhudza ubongo monga kuzungulira, kutafuna, ukali, kugwa ndikufa
- Ziweto zonse m’khola zimatha kufa.
- Ng’ombe zisambitsidwe ku dipi kapena zipatsidwe katemera wa matendawa
Kutupa kwa Ndulu (Anaplasmosis)
- Ng’ombe zazikulu zimadwalika nawo kwambiri kuposa zachichepere
- Ng’ombe zimasiya kudya, zimatentha thupi ndipo zimatulutsa mkaka ochepa
- Kuchepa kwa magazi ndipo thupi limaoneka la chikasu.
- Kuwonda komanso kudzimbidwa
- Kupuma mwa befu, kupoloza ndinso kudzandira
- Sipakhala mkodzo wofiira
- Chiweto chimafa pakatha sabata imodzi kapena kukhala ofooka nthawi yayitali.
- Ng’ombe zisambitsidwe ku dipi kapena zipatsidwe katemera wa matendawa
Matenda Ofiiritsa Mkodzo Ndikuzunguza Bongo (Babesiosis)
- Chiweto chimasiya kudya, chimatulutsa mkaka ochepa, chimatentha thupi.
- Kuchepa kwa magazi komanso thupi limaoneka la chikasu
- Imaonetsa zizindikiro za kusokonekera kwa ubongo
- Kufiira kwa mkodzo
- Kufa mwina kudwalika kwa masabata angapo.
- Ng’ombe zisambitsidwe ku dipi kapena zipatsidwe katemera wa matendawa.
Matenda Ogonetsa (Sleeping Sickness)
- Kutentha kwa thupi mpaka 41.5oC komwe kumakwera ndikutsika mmasiku ochepa
- Kusakhazikika komanso chilakolako cha chakudya chimachepa
- Kuchepa kwa magazi ndi kuwonda
- Kutuluka anabere
- Kupoloza.
- Musadyetsere kumalo komwe ku mapezeka ntchentche zikuluzikulu
- Yenderani ng’ombe zanu kuti muone ngati pali tizilomboti
- Ngati ng’ombe imodzi olo ziwiri zadwala m’mwezi umodzi, zipatseni mankhwala zonse kupewa kuti zingadwale.