MITUNDU YA NG'OMBE ZA MKAKA
MITUNDU YA NG’OMBE ZA MKAKA
Ng’ombe ya Malawi Zebu ndi ng’ombe yokhayo ya mkaka yachikuda, komabe imapereka mkaka wochepa. Alimi akulimbikitsidwa kukwatitsa ndi ng’ombe zachizungu kuti achulukitse mkaka.
Ubwino wa ng’ombe zachizungu
- Zimakula msanga komaso zimapereka mkaka wambiri
- Zimakhala ndi msinkhu waukulu komanso zimakha ndi nyama yambiri
- Zimagulitsidwa pamtengo wokwera
- Ndizofatsa komaso zosavuta kusamala.
Zovuta ku ng’ombe zachizungu
- Zimafuna ndalama zochuluka poyamba ulimiwu
- Zimafuna luso ndi upangiri wa padera
- Ndizosapirira kumatenda.
Ubwino wa ng’ombe zokwatitsa (Crosses)
- Ndizopirira kumatenda kuyerekeza ndi zachizungu
- Zimapereka mkaka wochuluka kuposa zachikuda
- Ndi za msinkhu wochepera kuyerekeza ndi zachizungu choncho zimafunaso chakudya chocheperako kuyerekeza ndi za chizungu.
Zovuta ku ng’ombe zokwatitsa (Crosses)
- Zimapereka mkaka wochepa poyerekeza ndi ng’ombe za chizungu
- Zimapereka mkaka wa mafuta ochepa poyerekeza ndi ng’ombe zachikuda
- Zimapereka mkaka kwa nthawi yochepa poyerekeza ndi ng’ombe za chizungu.
Mitundu ya ng’ombe za mkaka zovomerezeka ku Malawi ndi Friesian/Holstein, Malawi Zebu dairy crosses, Jersey ndi Aryshire.
Ng’ombe Zachizungu
Friesian-Holstein
- Imatha kuwetedwa ngati ng’ombe ya mkaka kapena ya nyama
- Imatha kulemera 400 kg mpaka 500kg
- Imakhala ndi mawanga okuda ndi oyera
- Ng’ombe imodzi imatha kupereka mkaka wokwanira malita 30 mpaka 40 pa tsiku
- Ndizofatsa kotero sizivuta kusamala.
Jersey
- Ndiyocheperako msinkhu kuyerekeza ndi Friesian/Holstein ndipo imalemera makilogalamu okwana 300 mpaka 400
- Imawoneka yofirirako pang’ono, komanso yoderako
- Zimakhala ndi mchira wakuda komanso bere lalikulu
- Zitha kupereka mkaka wokwanira malita 10 mpaka 15 patsiku ng’ombe imodzi
- Zimapereka mkaka wokhala ndi michere yomanga thupi (protein) yochuluka ngakhalenso michere ina.
Ayrshire
- Imaoneka yofirira yokhala ndi mawanga oyera
- Zimadya msipu mosavuta komanso zimapereka mkaka wambiri
- Ndiyofatsa kotero simavuta kusamala
- Imalemera 500kg mpaka 600kg
- Ng’ombe imodzi imatha kupereka mkaka wokwanira malita 15 mpaka 20 pa tsiku.
Malawian Zebu crosses.
Ndi mtundu okwatitsa Zebu ndi ng’ombe zina za chizungu ndi cholinga chakuti zizipereka mkaka wambiri. Mtunduwu umatha kupereka malita okwanira 10 mpaka 20 pa tsiku.