ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

UKHONDO NDI KUSAMALA MKAKA

UKHONDO NDI KUSAMALA MKAKA

Mukuyenera kuonesetsa kuti dongosolo lonse la ukhondo wa mkaka mukulitsatira pokama mkaka kuti muchepetse kutaya mkaka chifukwa chakuti waonongeka. Mkaka umakondedwanso ndi tizirombo tosiyanasiyana tosaoneka ndimaso, tomwe timaononga mkaka ndikupereka matenda kwa anthu omwe amwa mkakawu. Kuti mukame mkaka waukhondo, ndipofunika kutsatirazi zinthu izi;

  • Khola la ukhondo – Khola likhale losamalidwa bwino, losakhala ndi matope ndi zinyala. M’khola mukhale zogonera kuti ng’ombe ikhale yaukhondo ndiponso yotetezeka ku tizirombo topereka matenda. Malo okamira mkaka pansi pake pakhale pa simenti yosaterera kuti musamavutike kukonza
  • Wokama waukhondo – Munthu yemwe akukama mkaka akhale wathanzi, zala zowengedwa bwino, asambe m’manja komanso avale zovala zoyera ndi zaukhondo ndi chipewa. Wokamayu asakhale ndi matenda opatsirana pakati pa anthu ndi nyama.
  • Ng’ombe yaukhondo – Ng’ombe ikhale yathanzi ndi yaukhondo. Bere komanso nkhumbu muzitsuke bwino lomwe ndi madzi abwino ofunda ndi kuumitsa/kupukuta ndi kansalu koyera bwino
  • Ziwiya zaukhondo – Mkaka umayamba kusintha pa nthawi yomwe mwangomaliza kukama koma kuti mupewe izi, gwiritsani ntchito ziwiya zotsuka bwino potsatira ndondomeko iyi;
  1. Tsukuluzani ndi kuchotsa mkaka onse otsalira mu ziwiya ndi madzi aukhondo komanso ozizira
  2. Onetsetsani kuti ziwiya zonse mwakwecha bwino ndi madzi otentha komanso othira sopo
  3. Mukatero tsukuluzani ndi madzi ozizira aukhondo
  4. Mukamaliza kutsuka ziwiya, zivindikiridwe mozondoka pa malo oyanikira pa dzuwa.
  • Ndikofunika kwathunthu kusefa mkaka ndi kansalu koyera kaukhondo. Kansalu kosefera mkaka muzikachapa ndi sopo nthawi zonse mukamaliza kusefa
  • Muonetsetse kuti mkaka mwausunga malo ozizira kuti tizirombo tooletsa mkaka tisachulukane
  • Musaphatikize mkaka womwe mwakama m’mawa ndi womwe mwakama madzulo
  • Ngati ku dera lanu kuli malo osungilako mkaka (bulking group), kaperekeni mkaka wanu ku maloko panthawi yomwe mwangomaliza kukama.
Share this Doc