ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

ZINA ZOYENERA KUCHITIKA POSAMALA MATOLE

ZINA ZOYENERA KUCHITIKA POSAMALA MATOLE

Zinthu zotsatirazi muzipange pofuna kuti matole anu asamalidwe bwino. Izi muzichite mutatsala pang’ono kulekanitsa thole ndi mayi wake kapena mutangolekanitsa kumene mwana ndi mayi wake.

  • Chizindikiritso: Kuika ndolo kapena chidindo kuti thole lanu muzirizindikira bwino pochita kalembera
  • Kuchotsa nyanga: Gwiritsani ntchito chitsulo cha moto pootcha momwe mukuyamba kutuluka nyanga
  • Kuthena: Mugwiritse ntchito labala ozungulira kapena pulayala yopanira
  • Kumwetsa mankhwala a njoka za m’mimba: Gwiritsani ntchito mankhwala oyenerera othana ndi njoka za m’mimba
  • Kuthetsa nkhupakupa: Gwiritsani ntchito dipi ovomerezeka komanso njira yovomerezeka
  • Kuyeza kulemera kwa matole: Gwiritsani ntchito lamba wa muyezo kapena sikelo pofuna kuyeza kulemera kwa matole anu.

Matenda a ana a ng’ombe

MATENDA

ZIZINDIKIRO

KUPEWA NDI KUTETEZA

Chapamchombo

  • Pa mchombo pamatupa,
  • Amatentha thupi komanso
  • Sakhala ndi chilakolako cha chakudya
  • Malo oberekera ndi osungiramo ana a ng’ombe azikhala a ukhondo
  • Ana a ng’ombe asakhale m’makola a matope komanso onyowa.

Chibayo

  • Kutentha thupi komanso kubanika
  • Amatuluka mamina ndi misozi nthawi zina.
  • Ana ang’ombe asakhale ponyowa ndi pozizira.

Kutsegula M’mimba

  • Ndowe zimakhala za madzimadzi
  • Madzi a m’thupi amachepa
  • Imaoneka yosachangamuka
  • Imakhala yofooka, imadzandira ikamayenda ndipo imakanika kuima chiriri.
  • Onetsetsani kuti ana ang’ombe ayamwa mkaka oyambirira kutuluka (Chithuwi) akabadwa
  • Ana asungidwe padera osati pamodzi ndi zazikulu
  • Ana akhale m’khola la ukhondo ndi louma bwino.
Share this Doc