ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

ZOFUNIKIRA KU CHAKUDYA CHA NG’OMBE YA MKAKA

Zofunikira ku chakudya cha ng’ombe ya mkaka

  1. Kudyetsa msoti
  • Kufikira miyezi isanu ndi umodzi (6) yakubadwa, msoti mutha kumaudyetsa udzu okhaokha ngati udzuwo uli wabwino
  • Ngati zakudya zosakaniza zilipo, mutha kupereka zakudyazi zokwana kilogalamu imodzi (1) kapena awiri (2) tsiku lirilonse kuyambira pomwe msoti wanu wakwanitsa miyezi isanu ndi umodzi (6) kufika chaka chimodzi. Izi zimathandiza kuti msoti ukule bwino.
  1. Kudyetsa ng’ombe kapena msoti wa bere
  • Muyambe kuipatsa ng’ombe kapena msoti wanu zakudya zosakaniza pamene kwatsala miyezi iwiri kuti ibereke
  • Muzidyetsa chakudya chokwana pakati pa kilogalamu imodzi (1) ndi imodzi ndi theka (1.5) patsiku.
  1. Kudyetsa ng’ombe yokama
  • Kwa masiku atatu pomwe mwana wangobadwa, muipatse ng’ombe yanu chakudya chosakaniza chocheperako koma udzu khale ochuluka momwe ng’ombe ingadyere
  • Zakudya zosakaniza zokhala ndi michere ya protein yochulukirapo ziperekedwe ku ng’ombe yomwe imapereka mkaka wochuluka. Zakudyazi ziperekedwe pa mulingo wa 1kg ya chakudya pa 2.5Kg iliyonse ya mkaka wokamidwa
  • Ngati udzu usali wabwino kwenikweni, chakudya chosakaniza chikhale cha michere yomanga thupi / protein yochulukirapo
  • Mupereke madzi ambiri abwino ndi aukhondo ku ng’ombe yanu nthawi zonse.
  1. Kudyetsa ng’ombe yosakamidwa (yomwe mwasiya kukama)
  • Ngati ng’ombe yosakamidwa (yomwe mwasiya kukama) ili ndi thupi labwino mutha kuyidyetsa udzu womwe uli wabwino popanda chakudya china choonjezera
  •  Ng’ombe yomwe ili ndi thupi lonyentchera muipatse chakudya chosakaniza chokwana makilogalamu awiri (2kgs) tsiku lirilonse patangotha masabata awiri mutasiya kuikama mpaka pomwe kwatsala masabata awiri kuti ibereke
  • Muchepetse chakudya popereka kilogalamu imodzi (1kg) ya chakudya tsiku lirilonse pomwe kwatsala masabata awiri kuti ng’ombe ibereke.
  1. Kudyetsa nkhuzi

Ngati mukusunga nkhuzi yoti muzikweretsa ng’ombe zanu muyenera muziipatsa udzu wabwino kuonjezeraponso zakudya zosakaniza zochuluka pakati pa makilogalamu awiri (2kgs) ndi anayi (4kg) tsiku lirilonse. 

Share this Doc