KASAMALIDWE KA NJUCHI MU MNG'OMA
KASAMALIDWE KA NJUCHI MU MNG’OMA
Kuyendera Ndi Kuyang’anira Ming’oma
Zimathandiza mlimi wa njuchi kukonza mkati, monga zisa, kuchotsa kangaude ndi zina. Tsatirani fundo izi poyendera:
- Onetsetsani kuti manthu/mfumukazi akugwira bwino ntchito yake ndipo ali ndi thanzi
- Mlimi akamayendera ming’oma amadziwa nthawi ndi nyengo yokololera uchi. Nthawi yabwino yoyendera ming’oma ndi kum’mawa ndi kumadzulo koma osati ndi mdima
- Kuyang’ana tizilombo ndi tinyama towononga uchi kapena ming’oma
- Kuteteza kapena kuletsa kusamukasamuka kwa njuchi poonetsetsa zosoweka za njuchi monga madzi ndi zakudya zikupezeka.
Zopangitsa Njuchi kusamukamu mng`oma/pa malo
- Kusowa kwa chakudya
- Anthu osokoneza monga phokoso ndi kuwononga mng`oma
- Zinyama zodya uchi monga chiuli
- Mbewa, moto, kusintha kwa nyengo (kuzizira kwambiri, kutentha kwambiri, ndi mphepo yankuntho) ndi nyerere
- Kuchepa kwa malo mu mng’oma chifukwa cha kuchuluka kwa njuchi, ana anjuchi komanso zisa
- Kusatsatira njira zoyenera pakawetedwe ka njuchi monga kutsegula mng`oma popanda chouzira utsi.
Zizindikiro Zosonyeza Kuti Njuchi zisamuka Pa Malo
- kuchulukana kwa njuchi mu mng’oma.
- Njuchi zikakhala m’magulumagulu kunja kwa mng’oma kwa tsiku lonse
- Kuchepa kwa kuuluka kwa njuchi zimene zimagwira ntchito mu mng’oma
- Kusowa kwa madzi ndi chakudya.
Mmene Tingachepetsere Kuchoka Kwa Njuchi mng`oma
- Kupeza malo omwe pali mthunzi ndi zomera zokwanira
- Kuyendera ming’oma pafupipafupi
- Kudyetsera njuchi nthawi yosowa maluwa ndi zakudya
- Kuteteza ming’oma ku moto ndi tizilombo toononga