ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUKOLOLA UCHI

KUKOLOLA UCHI

Nthawi zambiri uchi umakololedwa kuyambira mwezi wa March mpaka August ndi December. Uchi wa March umakhala ndi madzi ambiri chifukwa zomera zambiri zimakhala ziri ndi maluwa. Nthawi yabwino yokolola uchi ndi kumadzulo. Ming’oma ikololedwe pamene tayendera ndi kukhutitsidwa kuti zinthu ziri bwino mu mng’omamo.

M’Malawi muno ming’oma imene anthu ambiri amagwiritsa ntchito ndi imene imakhala ndi timatabwa tomwe njuchi zimamanga chisa “top bars”. Pa mng’oma umodzi osamalidwa bwino mlimi amayenera kukolola uchi ochuluka 35Kgs kapena kuposera apa.

Zoyenera kuchita pokolola

  • Kusonkhanitsa zida ndi zipangizo zoyenera monga ndowa ndi zina. Zisa zikuyenera kuikidwa malo osiyana kutengera ndi kawonekedwe ka uchi oyenera kukololedwa. Izi zimathandiza ndi kukwaniritsa kukolola uchi wamaonekedwe abwino kuti usakavute malonda pa msika
  • Pokolola uchi pamafunika anthu awiri pa mng’oma umodzi, mpaka kumaliza kukolola. Anthuwa amayenera kuchita izi:
  • Munthu oyamba amanyamula chopepelera utsi (simoka), uyu ndi amene amafika koyambirira ndi kupopera pa mng’oma usanatsegulidwe komanso pomwe ukutsegulidwa. Izi zimapangitsa kuti njuchi zikhale zofooka pena kukomoka pamene ntchito yokolola iri mkati
  • munthu wachiwiriyo amatsegula mng’oma, wautsi akupepelerabe. Kenako amasiya ndikuyamba kukolola ndipo ngati zioneke kuti njuchi zikupeza mphamvu kapena kutsitsimuka amayenera kupoperanso utsi.

Chotsani / kololani zisa zonse zomwe zakhwima / zotsekera ndikusiya zomwe mudakali ana kapena zosakhwima. Ngati mng’oma onse uli ndi zisa zokhwima siyaniko timitengo titatu osakolola zonse kuopa njuchi kuthawa mu mng’oma.

Share this Doc