KULOWA KWA NJUCHI MU MING'OMA
KULOWA KWA NJUCHI MU MNG’OMA
Pali njira ziwiri zomwe njuchi zimaloweramu mng’oma.
1. Njira ya chilengedwe
Njuchi zimatha kulowa zokha mng’oma makamaka pakakhala pamalo abwino.
2. Njira yothandizidwa
- Mlimi amayika malesa, phula, masamba a mandimu kapena shuga mu mng’oma. Izi zimathandizira kuyitanira njuchi.
- Mlimi atha kusamutsa kapena kugwira njuchi kuchoka pomwe zamanga ndi kukayika mu mng’oma pogwiritsa ntchito thumba/saka losabooka.
Zolepheretsa Kuti Njuchi Zilowe Mung’oma
- Kupachika ming’oma m’malo wosayenera monga malo opanda mthunzi ndi malo odutsa mphepo kwambiri
- Kukhazika ming’oma nyengo yosayenera
- Kukhazika ming’oma yowonongeka
- Nyama ndi zouluka zolusa zimene ndi adani a njuchi
- Kukoza ming’oma ndimatabwa afungo loipa ngati a mtengo wa paini
- Kuyang`anitsa khomo mbali yomwe kumachokera mphepo.
Njira Ziwiri Zopachikira Mng’oma
- Pa mitemgo iwiri
- Kupachika pamwala / thandala lopangidwa ndi mitengo.
Pamitemgo iwiri
- Sankhani mitengo iwiri yaikulu bwino imene kutalikirana kwake kukhale ma mita 4 kapena 5
- Lambulani pa malowo komanso dulani nthambi zonse zamitengo zimene zikukhudza mng’oma
- Dulani waya otalika theka la mita imodzi ndikupanga magonga (loops) awiri.
- Tengani magonga awiri, koletsani ndikumanga ku mitengo iwiri
- Dulani waya potengera kutalikirana kwa mitengo iwiri
- Pisitsani mawaya awiriwo mkati mwa mng’oma
- Mangani magongawa 5 cm kuchokera ku ming’oma pamakona anayi
- Ikani mng’oma wanu pakati pa mitengo iwiri ndipo khomo la mng’oma liyang’ane mbali kumene mphepo siyikupita
- Tengani waya adzere ndikukoletsa mu gonga ndikumanga mozungulira mitengo iwiriyo
- Mng’oma ukhale otalika mita imodzi kuchokera pansi poteteza kuti kanyama kotchedwa Chiuli (honey badger) kuti kasawononge mng’oma ndi njuchi
- Mng’oma ukhale mwa fulati ndi kumanga waya pogwiritsa ntchito magonga aja
- Ikani nyambo yokopa njuchi pamwamba pa matabwa (top bars) ndi mkati mwa mng’oma
- Pakani girizi ku waya poteteza nyerere ndi chiswe kuti zisalowe mu mng’oma
- Ming’oma yanu muipatse manambala ndikulemba mu bukhu kapena pepala, losungiramo malekodi. Izi zimathandiza kupanga kalondolondo mosavuta
- Ming’oma ipachikidwe m’nyengo kapena nthawi imene njuchi zikuuluka m’magulumagulu.
Mng’oma opachikidwa pa mitengo iwiri
Kupachika pamwala/ Thandala lopangidwa ndi mitengo
Mangani thandala losaposera 1 mita, ndipo muonetsetse kuti thandala lanu liyime mofanana mbali zonse osati lopendekeka. Thandala limangidwe poganizira njira zonse zotetezera zilombo zoononga uchi.