ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MATENDA NDI TIZILOMBO TA NJUCHI

MATENDA NDI TIZILOMBO TA NJUCHI

Zinyama Zosautsa Njuchi ndi kapewedwe kake

Zinyama tosautsa ku njuchi ndi monga izi:

    Chiuli, kanyama kodya uchi, (Honey Badger)

  • Pachikani mng’oma 1m kuchoka pansi pakati pa mitengo iwiri yotalikirana 5m
  • Chotsani kapena dulani nthambi za mitengo zimene zikukhudza mng’oma kuchokera ku mwamba kwa mtengo.

    Chiswe ndi Nyerere

  • Pakani girizi mawaya amene agwirana ndi mng’oma kawiri kawiri
  • Wazani phulusa pansi pa mitengo pamene pali mng’oma
  • Chotsani udzu onse umene uli pansi pa mitengo mwayika mng’oma.

    Gulugufe (Wax moth)

  • Ana a gulugufe (mbozi) amaononga malesa makamaka momwe muli ana a njuchi. Pangani izi kuti muthane ndi vutoli:
  • Zulani / chotsani zisa zonse mu mng’oma zimene mulibe kanthu
  • Tsukani timatabwa tomwe njuchi zimamangapo chisa “Top Bars” tomwe takololedwa.

 

    Anthu akuba

  • Alimbikitseni anthu ena kutenga nawo gawo pa ulimi wanjuchi
  • Ming`oma isakhale kutali kwambiri ndi nyumba zokhala anthu
  • Yenderani ming`oma pafupipafupi.
Share this Doc