ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MITUNDU YA NJUCHI

MITUNDU YA NJUCHI

Zunguya, mfumukazi and ogwira ntchito (source: www.pinterest.com)

    Zunguya (drone)

  • Iyi ndi njuchi yaimuna yomwe imagonana ndi manthu
  • Thupi lake ndi lokhuthala ndi lakuda
  • Ilibe mbola komanso ilibe mano
  • Ili ndi maso akuluakulu
  • Moyo wake imakhala masiku sikisite
  • Imafa ikagonana ndi manthu kapena nthawi yanjala imantha kuphedwa ndiogwirira ntchito.

    Mfumukazi / Manthu (Queen)

  • Ili ndi fungo lonukhira bwino lomwe limaitana amuna.
  • Mapiko ake ndioyerelako komanso atalikirako
  • Khosi lake ndilokulirako ndiponso laubweya waufupi.
  • Ilibe miyendo yotengela ufa.
  • Imaikila mazira 2500 kapena kuposela apo pa dziku
  • Moyo wake umakhala pakati pa zaka ziwiri ndi zisanu
  • Mkamwa mwake mulibe mano.
  • Mazira amatenga masiku atatu kuti igogomole

    Ogwira ntchito (workers)

  • Imaikira mazira koma sagogomola
  • Ili ndi zida zonse zokwanila kugwiritsira ntchito pokatenga ufa wa mmaluwa, madzi, phula.
  • Njuchi izi zimakhala ndiubweya komanso matupi ake amakha onyata
  • Iyi ndiimene imagwira ntchito zones ming’oma monga; kuteteza ana anjuchi nzisa, kusamalira mabokosi momwe muli ana anjuchi, kupeza zakudya.
Share this Doc