NDONDOMEKO YOYENERA KUTSATA MUKAFIKA PA MNG'OMA PA NTHAWI YOYENDERA KAPENA KUKOLOLA
NDONDOMEKO YOYENERA KUTSATA MUKAFIKA PA MNG’OMA PA NTHAWI YOYENDERA KAPENA KUKOLOLA
Musanafike Pa Mng’oma
- Muyime kaye patali ndi kuvala zovala zoyenera (bee suit)
- Muwonetsetse kuti chofukizira utsi chikuyaka bwino ndipo kuti muli ndi zoyatsira zokwanira. Kawirikawiri zoyatsira zabwino ndi ndowe zang’ombe kapena zitsononkho ndipo onetsetsani kuti zikhale zouma
- Fikani pa mng’oma kudzera kumbuyo osati kutsogolo kumene kuli khomo.
Pa Mng’oma
- Munthu amene ali ndi chofukizira utsi ndi amene apite kutsogolo kwa mng’oma
- Poperani utsi mu mng’oma
- Atagwira ntchito yopopera utsi mu mng’oma, munthuyo achoke ndikupita kumbuyo kumene kuli anzake kuti nawo apeze mpata ogwira ntchito.
Zosayenera Kuchita Mukafika Pa Mng’oma
- Osatsekula mng’oma popanda chifukwa koamnso osasiya mng’oma wotseguka nthawi yayitali
- Osafika pa mng’oma ndi chofukizira utsi chimene sichikuyaka bwino
- Osagwiritsa ntchito moto oyaka kuopa kuotcha njuchi
- Osafika pafupi ndi mng’oma musanavale -zovala zozitetezera
- Osayima kutsogolo kwa mng’oma
- Osapanga phokoso pamene mukugwira ntchito pa mng’oma
- Osapita kumene kuli ming’oma ya njuchi mutadzola kapena kunyamula mafuta wonunkhira (perfurme)
- Osatsegula ming’oma nthawi ya usiku
- Osavala zovala za ubweya komanso zokhwepa pa mng’oma
- Osagwiritsa ntchito matayala, machubu, makatoni amene adatengeramo zinthu za poizoni